Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ndise Banja Lanu

Ndise Banja Lanu

Daunilodi:

  1. 1. Tafika kumalo ena tacokeladi kutali.

    Ulendo wonse tiyamikila madalitso a M’lungu.

    Olo nchitoyi siyopepuka, ticitila Yehova.

    Cikondi cathu ni cazoona, conco tikunena kuti:

    (KOLASI)

    Ndise anthu a M’lungu, pamodzi ndisedi banja.

    Ngakhale muli kutali, dziŵani tikukondani.

  2. 2. Munali kuyembekeza kuti tipatsane moni

    Nyimbo zayamba pa misonkhano m’gwilizano ulimba

    Yehova ndiye amapangitsa kuti tigwilizane

    Tidzamutamanda mpaka kumalekezelo adziko lonse

    (KOLASI)

    Ndise anthu a M’lungu, pamodzi ndisedi banja.

    Ngakhale muli kutali, dziŵani tikukondani.

  3. 3. Tinawolokanso nyanja kubwela kumalo ano.

    Kuti tilalikile kwa anthu ofuna kumvetsela.

    Timamasukanso tikaona, cikondi ca abale.

    Conco, kulikonse tingayende tikonda abale onse.

    (BILIJI)

    Tikondwela kupeza banja konse tingayende

    Ku Mali, ku Mexico, ku Japan na ku Congo.

    (KOLASI)

    Ndise anthu a M’lungu, pamodzi ndisedi banja.

    Ngakhale muli kutali, dziŵani tikukondani.

    Mitundu yonse m’dziko, pamodzi ndisedi banja.

    Timaonetsa cikondi, ndisedi banja la Yehova.

    India, Colombia na ku Madagascar.

    Russia, Tahiti na Malawi,

    Azerbaijan, Kazakhstan, na Estonia.

    Dziŵani, tikukondani!