Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

2 | “Malemba . . . Amatilimbikitsa”

2 | “Malemba . . . Amatilimbikitsa”

BAIBO IMATI:“Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. ­Malembawa amatipatsa ciyembekezo cifukwa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.”—AROMA 15:4.

Tanthauzo Lake

M’Baibo muli mfundo zolimbikitsa, zimene zingatithandize tikakhala na maganizo olefula. Komanso Baibo imatipatsa ciyembekezo cakuti posacedwa, zinthu zopweteka mtima zidzatha.

Mmene Zimenezi Zingatithandizile

Tonsefe nthawi zina timakhala osakondwa. Koma anthu odwala matenda opsinjika maganizo kapena ankhawa, angamakhale owawidwa mtima nthawi zonse. Kodi Baibo ingawathandize bwanji?

  • M’Baibo muli mfundo zambili zolimbikitsa zimene zingatithandize kucotsa maganizo olefula mumtima mwathu (Afilipi 4:8) Baibo ingadzaze mitima yathu na maganizo otonthoza komanso otsitsimula, amene angatikhazike mtima pansi.—Salimo 94:18, 19.

  • Baibo imatithandiza kuthetsa maganizo odziona ngati osafunika.—Luka 12:6, 7.

  • M’Baibo muli malemba ambili amene amatitsimikizila kuti sitili tokha, komanso kuti Mlengi wathu Mulungu amamvetsa mmene tikumvela.​—Salimo 34:18; 1 Yohane 3:19, 20.

  • Baibo imalonjeza kuti Mulungu adzathetsa zowawa zonse, moti sizidzakumbukilidwanso. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4) Tikakhala na nkhawa, mantha, kapena cisoni, komanso tikamavutika maganizo cifukwa ca mavuto amene tikukumana nawo, lonjezo limeneli lingatithandize kupilila.