Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amathandiza

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amathandiza

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amathandiza

MFUMU DAVIDE ankavutika maganizo kwambiri ndipo anali ndi “zolingalira” zambiri zimene zinkamusowetsa mtendere. Komabe iye sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Mlengi amadziwa zimene timakumana nazo. Iye anati: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali. Pakuti asanafike mawu pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziwa onse.”—Salmo 139:1, 2, 4, 23.

Ifenso sitikayikira kuti Mlengi wathu amatidziwa bwino ndiponso amadziwa mavuto amene tikukumana nawo chifukwa cha matenda ovutika maganizo. Iye amadziwa zimene zimayambitsa matendawa ndi mmene tingawapiririre. Komanso amatiuza mmene adzawathetsere. Palibe munthu wina amene angatithandize kuposa Mulungu wathu wachifundo, amene “amatonthoza osautsika mtima.”—2 Akorinto 7:6.

Anthu amene akudwala matenda ovutika maganizo angafune kudziwa mmene Mulungu angawathandizire.

Kodi Mulungu amamva mapemphero a anthu amene akuvutika maganizo?

Mulungu ali pafupi kwambiri ndi atumiki ake amene ali ndi matenda ovutika maganizo, moti amakhala ngati ali pamodzi ndi “yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.” (Yesaya 57:15) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”—Salmo 34:18.

Kodi anthu ovutika maganizo angatani kuti Mulungu awathandize?

Anthu amene amalambira Mulungu angathe kupempha “Wakumva pemphero” nthawi ina iliyonse kuti awathandize kulimbana ndi matenda ovutika maganizo. (Salmo 65:2) Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziuza Yehova zakukhosi kwathu. Limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.

Bwanji ngati tili ndi maganizo akuti ndife osafunika ndipo Mulungu sangamve mapemphero athu?

Chifukwa cha kuvutika maganizo, tingaganize kuti palibe chomwe tingachite kuti tisangalatse Mulungu. Koma Atate wathu wakumwamba amadziwa maganizo athu ndipo ‘amakumbukira kuti ndife fumbi.’ (Salmo 103:14) Ngakhale kuti “mitima yathu ingatitsutse,” “tidzatsimikizira mitima yathu” kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Choncho popemphera mungagwiritse ntchito mawu amene munawerenga m’Baibulo, monga Salmo 9:9, 10; 10:12, 14, 17; ndi 25:17.

Bwanji ngati mukulephera kufotokoza maganizo anu?

Ngati mukuvutika kwambiri maganizo moti mukulephera kufotokoza maganizo anu, musataye mtima. Pitirizani kupemphera kwa “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu wachitonthozo chonse,” chifukwa iye amadziwa mmene mukumvera ndi zimene mukufuna. (2 Akorinto 1:3) Maria, yemwe tinamutchula m’nkhani zoyambirira uja, anati: “Nthawi zina, ndikasokonezeka kwambiri maganizo, ndimasowa mawu oti ndinene m’pemphero. Koma ndimakhulupirira kuti Mulungu amadziwa mmene ndikumvera ndipo amandithandiza.”

Kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphero athu?

Baibulo silinena kuti Mulungu amachotsa mavuto onse panopa. Koma limanena kuti Mulungu amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira “zinthu zonse,” kuphatikizapo matenda ovutika maganizo. (Afilipi 4:13) Martina anati: “Nditayamba kudwala matenda ovutika maganizo, ndinapemphera kwa Yehova kuti andichiritse nthawi yomweyo, chifukwa ndinkaganiza kuti sindingathe kuwapirira. Panopa ndimangopempha kuti tsiku lililonse azindipatsa mphamvu kuti ndithe kupirira.”

Malemba amalimbikitsa kwambiri anthu amene akuvutika maganizo. Sarah, amene wakhala akudwala matendawa kwa zaka 35, anaona kuti kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku n’kothandiza kwambiri. Iye anati: “Ndimathokoza madokotala pa zimene andichitira. Koma kuwerenga Mawu a Mulungu n’kumene kwandithandiza kwambiri. Ndimawerenga Baibulo tsiku lililonse.”

Kuvutika Maganizo Kudzatha

Yesu Khristu ali padziko lapansi anasonyeza kuti Mulungu anamupatsa mphamvu zochiritsira matenda. Iye anali wofunitsitsa kuthandiza anthu amene anali ndi matenda aakulu. Ndiponso Yesu pa nthawi ina anavutikapo maganizo kwambiri. Usiku woti aphedwa, “Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha, kwa Iye amene anali wokhoza kum’pulumutsa ku imfa. Anawapereka ndi kulira kwakukulu ndi misozi.” (Aheberi 5:7) Mavuto amene iye anakumana nawo, amamuchititsa kuti ‘azitha kuthandiza iwo amene akuyesedwa.’—Aheberi 2:18; 1 Yohane 2:1, 2.

Baibulo limatiuza kuti Mulungu adzachotsa zinthu zonse zimene zimatichititsa kuvutika maganizo. Iye analonjeza kuti: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ichi ndichilenga.” (Yesaya 65:17, 18) Mawu akuti “kumwamba kwatsopano” amatanthauza Ufumu wa Mulungu. Ufumuwu udzabweretsa “dziko lapansi latsopano,” lomwe ndi anthu olungama a padziko lapansi. Anthu amenewa sadzadwalanso matenda aliwonse ndipo adzakhala paubwenzi ndi Mulungu. Matenda onse adzatheratu.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m’dzenje lapansi; munamva mawu anga; musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine. Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati Usaope.”—Maliro 3:55-57

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

“LANKHULANI MOLIMBIKITSA KWA A MTIMA WACHISONI”

Barbara ali ndi matenda ovutika maganizo ndipo nthawi zambiri amadziona kuti ndi wosafunika. Matendawa akakula Barbara ndi mwamuna wake amaimbira foni Gerard, yemwe ndi mnzawo komanso ndi mkulu mumpingo. Gerard amamvetsera moleza mtima Barbara akamalira ndi kumufotokozera maganizo ake, ngakhale kuti Barbara amachita zimenezi mobwerezabwereza.

Barbara akamalankhula, Gerard amamvetsera moleza mtima popanda kumuweruza, kumutsutsa ndiponso kumudzudzula. (Yakobe 1:19) Iye amatsatira zimene Baibulo limanena kuti “lankhulani molimbikitsa kwa a mtima wachisoni.” (1 Atesalonika 5:14) Gerard moleza mtima amamuuza Barbara kuti iye ndi munthu wofunika kwambiri kwa Yehova Mulungu, kwa anthu a m’banja lake ndiponso kwa anzake. Nthawi zambiri Gerard amamuwerengera Barbara mavesi angapo a m’Baibulo, ngakhale kuti mavesi ena amakhala kuti anamuwerengerapo kale. Kenako, amapemphera naye, limodzi ndi mwamuna wake, pafoni pomwepo. Zimenezi zimalimbikitsa kwambiri banjali.—Yakobe 5:14, 15.

Gerard amadziwa kuti iye si dokotala, ndipo sayesa n’komwe kutenga udindo wa dokotala. Komabe kuwonjezera pa mankhwala amene Barbara amalandira, Gerard amamuchitira zinthu zimene madokotala ambiri sachita. Iye amamuwerengera malemba ndi kupemphera naye, ndipo zimenezi zimamutonthoza kwambiri.

Kuti ‘Mulankhule Molimbikitsa kwa a Mtima Wachisoni’

Munganene kuti: “Ndikufuna mungodziwa kuti ndakhala ndikukuganizirani. Kaya panopa mukupeza bwanji?”

Dziwani izi: Lankhulani mochokera pansi pa mtima ndipo mvetserani moleza mtima, ngakhale wodwalayo atamabwereza zimene anakuuzani kale.

Munganene kuti: “Ndimasangalala ndi zimene mumachita (kapena “makhalidwe anu abwino amene mumasonyeza”) ngakhale kuti mukudwala. Mwina mungaone ngati simukuchita zambiri, koma dziwani kuti Yehova amakukondani ndipo amayamikira zimene mukuchita. Ifenso timakukondani ndipo timakuyamikirani.

Dziwani izi: Khalani woleza mtima ndiponso wachifundo.

Munganene kuti: “Ndinapeza lemba lolimbikitsa kwambiri ili.” Kapena “Pamene ndimawerenga vesi limene ndimalikonda, ndinaganizira kwambiri za inuyo.” Kenako werengani vesilo, kapena kuligwira mawu.

Dziwani izi: Pewani kulankhula ngati mukumulalikira.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Malemba Amatonthoza

Lorraine amalimbikitsidwa ndi lonjezo la Yehova lopezeka pa lemba la Yesaya 41:10, lakuti: “Usawope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usawopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; ine, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.”

Álvaro ananena kuti mawu a pa Salmo 34:4, 6 amamutonthoza. Lembali limati: “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse. Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nam’pulumutsa m’masautso ake onse.”

Naoya ananena kuti akawerenga lemba la Salmo 40:1, 2 amalimbikitsidwa. Lembali limati: “Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Ndipo anandikweza kunditulutsa m’dzenje la chitayiko, ndi m’thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.”

Lemba la Salmo 147:3 limamulimbikitsa Naoko. Lembali limanena kuti Yehova “achiritsa osweka mtima, namanga mabala awo.”

Mawu a Yesu opezeka pa lemba la Luka 12:6, 7 amathandiza Eliz kukhulupirira kuti Yehova amatisamalira. Lembali limati: “Mpheta zisanu amazigulitsa makobili awiri ochepa mphamvu, si choncho nanga? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imaiwalika kwa Mulungu. Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu analiwerenga. Musachite mantha; ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.”

Mavesi ena olimbikitsa:

Salmo 39:12: “Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga.”

2 Akorinto 7:6: Mulungu “amatonthoza osautsika mtima.”

1 Petulo 5:7: ‘M’tulireni nkhawa zanu zonse [Mulungu], pakuti amasamala za inu.’