Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Tingathandizile Odwala Matenda a Maganizo

Mmene Tingathandizile Odwala Matenda a Maganizo

BAIBO IMATI: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—MIYAMBO 17:17.

Tanthauzo Lake

Tingathedwe nzelu ngati mnzathu akudwala matenda a maganizo. Koma tingaonetse kuti timam’konda mwa kum’thandiza kupilila vuto lakelo. Kodi tingamuthandize motani?

Mmene Zimenezi Zingathandizile

“Munthu aliyense akhale wofulumila kumva.”—YAKOBO 1:19.

Njila imodzi yabwino kwambili imene mungathandizile mnzanu wodwala matenda a maganizo ni kumumvetsela akafuna kukamba nanu. Musaganize kuti muyenela kunenapo kanthu pa ciliconse cimene iye wakamba. Onetsani kuti mukumvetsela zimene akukamba komanso kuti mumasamala za iye. Muziyesetsa kumvetsa mmene iye akumvela, ndipo pewani kumuweluza. Kumbukilani kuti mnzanuyo angakambe zinthu mosaganiza bwino, ndipo angadziimbe nazo mlandu pambuyo pake.—Yobu 6:2, 3.

“Lankhulani molimbikitsa.”—1 ATESALONIKA 5:14.

Mnzanu wodwala matenda a maganizo angakhale na nkhawa, kapena angamavutike na maganizo odziona ngati wosafunika. Conco, muyenela kum’tsimikizila kuti mumam’konda. Mukatelo, mungamutonthoze na kum’limbikitsa, ngakhale kuti simudziŵa mawu eni-eni amene mungakambe.

“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”—MIYAMBO 17:17.

M’thandizeni mnzanuyo pa zimene akufunikila. M’malo moganiza kuti mudziŵa mmene mungamuthandizile, mufunseni zimene mungacite pomuthandiza. Ngati mnzanuyo zikumuvuta kufotokoza zimene akufunika, yesani kupeleka malingalilo a zinthu zimene mungacitile pamodzi, monga kupita kokayenda. Kapena mungamuthandizeko kukagula zinthu, kuyeletsa, kapena nchito zina.—Agalatiya 6:2.

“Khalani oleza mtima.”—1 ATESALONIKA 5:14.

Si nthawi zonse pamene mnzanu angakhale wokonzeka kulankhula. Conco, muuzeni kuti ndinu wokonzeka kumumvetsela nthawi iliyonse imene angafune kukamba nanu. Cifukwa ca matenda ake, mnzanu angakambe kapena kucita zinthu zina zimene zingakukhumudwitseni. Iye angasinthe maganizo pa zinthu zimene munagwilizana kucitila limodzi komanso angakhumudwe. Koma khalani oleza mtima, ndiponso muzimumvetsa pamene mukumuthandiza.—Miyambo 18:24.

Zocita Zanu Zingamuthandize Mnzanu

“Nimayesetsa kukhala bwenzi lodalilika kwa mnzanga amene ali na vuto la kadyedwe komanso matenda ena a maganizo. Ngakhale kuti siningathetse mavuto ake, nthawi zonse nimamvetsela mwacidwi akafuna kukamba nane. Nthawi zina, mnzangayo amangofuna munthu womumvetsela kuti amveko bwino.”—Farrah, a amene mnzake ali na vuto la kadyedwe komanso matenda a kuda nkhawa kwambili na kupsinjika maganizo.

“Mmodzi wa anzanga ni wokoma mtima komanso wolimbikitsa. Ananiitanila ku cakudya cokoma ku nyumba kwake. Kumeneko, ananilandila mwacikondi komanso mokoma mtima. Zimenezi zinanipangitsa kuti nimasuke kufotokoza za kukhosi kwanga, ndiponso zinanilimbikitsa kwambili!”—Ha-eun, amene ali na matenda opsinjika maganizo.

“Kuleza mtima n’kofunika kwambili. Ngati mkazi wanga wacita cinacake conikhumudwitsa, nimakumbukila kuti wacita zimenezo cifukwa ca matenda ake, osati kuti ni mmene alili. Izi zimanithandiza kuti nisamukwiyile, koma m’malomwake nizicita zinthu momuganizila.”—Jacob, amene mkazi wake ali na matenda opsinjika maganizo.

“Mkazi wanga wakhala akunithandiza na kunilimbikitsa kwambili. Pamene nili na nkhawa kwambili, iye sanikakamiza kucita zinthu zimene sinikufuna. Izi zimapangitsa kuti nthawi zina asacite zinthu zimene akanakonda kucita. Mzimu wake wodzimana komanso kuwoloŵa manja kwake n’zamtengo wapatali.”—Enrico, amene ali na matenda a kuda nkhawa kwambili.

a Maina ena asinthidwa.