Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 8

Mafanizo Ophunzitsadi Kanthu

Mafanizo Ophunzitsadi Kanthu

Mateyu 13:34, 35

ZOFUNIKILA: Phunzitsani mwaluso pogwilitsila nchito mafanizo osavuta kumva kwa omvela anu, komanso kumveketsa mfundo zofunika.

MOCITILA:

  • Sankhani mafanizo osavuta. Monga mmene Yesu anacitila, gwilitsilani nchito zinthu zing’ono-zing’ono kumveketsa zinthu zikulu-zikulu, komanso zinthu zosavuta kumveketsa zinthu zovuta. Musaphatikizepo mbali zina zosafunikila kweni-kweni zimene zingacolowanitse fanizolo. Onetsetsani kuti fanizo limenelo likugwilizanadi na mfundo imene mufuna kuphunzitsa, kuti musawasokoneze omvela anu.

  • Ganizilani omvela anu. Sankhani mafanizo ophatikizapo zinthu zokhudza omvela anu. Koma samalani kuti mafanizo anu asakhale ocititsa manyazi omvela anu, kapena oŵakhumudwitsa.

  • Phunzitsani mfundo zazikulu. Mafanizo anu aziphunzitsa mfundo zazikulu, osati tumbali tocepa. Onetsetsani kuti omvela anu asakakumbukile fanizo cabe, koma maka-maka phunzilo lake.