Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 7

Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa

Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa

Luka 1:3

ZOFUNIKILA: Muzitenga mfundo zanu ku magwelo odalilika kuti omvela anu azikhutila nazo.

MOCITILA:

  • Pezani magwelo odalilika. Mfundo zanu zizitsamila pa Mawu a Mulungu. Ngati n’kotheka, ŵelengani mwacindunji. Ngati muchula mfundo yokhudza za sayansi, nkhani ya pa nyuzi, kapena cocitika cina cake, kapenanso umboni wina wake, tsimikizilani pasadakhale kuti magwelo anu ni odalilika komanso ni azoona.

  • Gwilitsilani nchito magwelowo moyenelela. Fotokozani malemba mogwilizana na nkhani yake, uthenga wonse wa m’Baibo, komanso na zofalitsa za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Ngati mugwilitsila nchito umboni wocokela ku magwelo akunja, useŵenzetseni mogwilizana na magwelo ake, komanso colinga ca wolemba wake.

  • Kambilanani umboni. Mukaŵelenga lemba kapena kuchula gwelo linalake, funsani mafunso mwaluso, kapena chulani citsanzo cothandiza omvela kuona mfundo yanu.