Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 11

Kukamba Mwaumoyo

Kukamba Mwaumoyo

Aroma 12:11

ZOFUNIKILA: Muzikamba mwaumoyo kuti omvela anu akhale ogalamuka komanso olimbikitsidwa.

MOCITILA:

  • Kambani mocokela pa mtima. Pokonzekela nkhani kapena ulaliki wanu, ganizilani za kufunika kwa uthenga wanu. Idziŵeni bwino nkhani yanu cakuti mukaikambe mocokela pa mtima.

  • Ganizilani omvela anu. Ganizilani za mmene mfundo zimene mudzaŵelenga kapena kuphunzitsa zingapindulitsile ena. Onani njila imene mungazifotokozele mowafika pa mtima omvela anu.

  • Ikani umoyo m’nkhani yanu. Kambani mwaumoyo, osati mopola. Pangani magesca acibadwa, komanso nkhope izionetsa mmene mukumvelela.