Onani zimene zilipo

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kupatsa?

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kupatsa?

Yankho la m’Baibo

 Baibo imatilimbikitsa kukhala opatsa, ndipo imati tizicita zimenezi na zolinga zabwino komanso osati mokakamizika. Imaonetsa kuti kupatsa koteloko kumapindulitsa wolandila ngakhalenso kwa wopelekayo. (Miyambo 11:25; Luka 6:38) Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Machitidwe 20:35.

 Ni kupatsa kotani kumene Mulungu amakondwela nako?

 Mulungu amakondwela tikamapatsa ena zinthu mwa kufuna kwathu. Baibo imati: “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”—2 Akorinto 9:7.

 Kupatsa na mtima wonse ni mbali ya “kupembedza” kumene Mulungu amavomeleza. (Yakobo 1:27) Yehova amakondwela na munthu amene amathandiza anthu moolowa manja. . Iye amaona kuti ali na nkhongole kwa munthuyo amene wathandiza ena. (Miyambo 19:17) Ndipo Baibo imati Mulungu adzabweza yekha ngongoleyo.—Luka 14:12-14.

 Ni kupatsa kotani kumene Mulungu sakondwela nako?

 Ngati munthu akupeleka na colinga cadyela. Mwacitsanzo:

  •   Pofuna kudzionetsela.—Mateyu 6:2.

  •   Pofuna kuti nayenso adzapatsidwe kena kake.—Luka 14:12-14.

  •   Pofuna kugula cipulumutso.—Salimo 49:6, 7.

 Ngati akupeleka pofuna kuthandizila pa zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Mwacitsanzo, si nzelu kupatsa munthu ndalama kuti akachovele njuga, kapena kukagulila mankhwala osokoneza bongo komanso kuti akamwe mowa n’kuledzela. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1) Komanso, si canzelu kupatsa ndalama munthu amene angakwanitse kugwila nchito na kudzipezela yekha zinthu zofunika koma amacita ulesi.—2 Atesalonika 3:10.

 Ngati zikupangitsa wopelekayo kunyalanyaza udindo wosamalila banja lake. Baibo imati amuna okwatila ayenela kusamalila mabanja awo. (1 Timoteyo 5:8) Conco, sicingakhale coyenela kuti mwamuna azipeleka zinthu zambili kwa anthu ena cakuti banja lake likusoŵa zinthu zina zofunikila. Yesu anadzudzula anthu amene anali kulephela kusamalila makolo awo okalamba pokamba kuti cuma cawo conse ni “mphatso yopelekedwa kwa Mulungu.”—Maliko 7:9-13.