Onani zimene zilipo

Kodi Mipingo Yanu Imayendetsedwa Bwanji?

Kodi Mipingo Yanu Imayendetsedwa Bwanji?

Mumpingo uliwonse mumakhala bungwe la akulu limene limatsogolela mpingo ndipo dela lililonse limakhala ndi mipingo pafupifupi 20. Pambuyo pa miyezi ingapo, mpingo uliwonse umayendeledwa ndi mkulu amene amacedwa woyang’anila dela.

Malangizo a m’Baibulo amacokela ku Bungwe Lolamulila lopangidwa ndi Mboni zimene zatumikila Yehova kwa nthawi yaitali. Bungwe limeneli limagwilila nchito ku likulu la Mboni za Yehova la padziko lonse ku Brooklyn, mumzinda wa New York.—Machitidwe 15:23-29; 1 Timoteyo 3:1-7.