Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 14

Tamandani Mfumu Yatsopano Yodzalamulila Dziko

Tamandani Mfumu Yatsopano Yodzalamulila Dziko

(Salimo 2:12)

  1. 1. Anthu amitundu yonse asonkhana pamodzi,

    Waaitana ni Khristu na odzozedwa ake.

    Ufumu wa M’lungu wathu;

    Tsopano ulamulila.

    Tipempha cifunilo cake,

    Cicitike na padziko.

    (KOLASI)

    Tamandani Yehova; tamandani Yesu—

    Mfumu ya Mafumu onse.

    Capamodzi timuimbile iye

    Ni Mfumu yosatha.

  2. 2. Titamanda Khristu Mfumu yathu, mosangalala.

    Ni Kalonga wa Mtendele adzatipulumutsa.

    Taonani madalitso

    Ufumu udzabweletsa;

    Yesu adzautsa akufa.

    Tidzalumpha mokondwela!

    (KOLASI)

    Tamandani Yehova; tamandani Yesu—

    Mfumu ya Mafumu onse.

    Capamodzi timuimbile iye

    Ni Mfumu yosatha.

(Onaninso Sal. 2:6; 45:1; Yes. 9:6; Yoh. 6:40.)