Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 61

Mtundu wa Munthu Amene Muyenera Kukhala

Mtundu wa Munthu Amene Muyenera Kukhala

(2 Petulo 3:11)

1. Ndithokoze bwanji, ndiperekenji

Kwa inu Yehova chifukwa cha moyo?

Mtima wangawu ndifuna ndiudziwe

Mawu anu Yehova andithandize.

Ndakulonjezani kukhala wanu.

Chifuniro chanu ndichita mwachangu

Ndasankhatu ndekha kutumikira,

Ndisangalatse inu Yehova.

2. Ndithandizenibe kudzifufuza

Ndikhaledi munthu amene mufuna.

Anthu otero mudzawasamalira

Kukhala mmodzi wa iwo ndakhumbira.

(Onaninso Sal. 18:25; 116:12; 119:37; Miy. 11:20.)