Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 27

Khalani ku Mbali ya Yehova

Khalani ku Mbali ya Yehova

(Eksodo 32:26)

1. Kale tinalitu achisoni,

Pokhala m’chipembedzo chonyenga;

Koma tinasangalala zedi

Titamva za Ufumu.

(KOLASI)

Yenda ndi Yehova

Umunyadire.

Khala mbali yake

Sangakusiye.

Lengeza uthenga

Wamtenderewu.

Ufumu wa Khristu

Sudzatha konse.

2. Tsopano tikusangalaladi

Ndi kufesa mbewu za cho’nadi.

Dzina la Yehova kukwezadi

Limodzi ndi abale.

(KOLASI)

Yenda ndi Yehova

Umunyadire.

Khala mbali yake

Sangakusiye.

Lengeza uthenga

Wamtenderewu.

Ufumu wa Khristu

Sudzatha konse.

3. Mdyerekezi sitidzamuopa,

Ife timadalira Yehova.

Adani akhoza kuchuluka,

M’lungu ndi mphamvu yathu.

(KOLASI)

Yenda ndi Yehova

Umunyadire.

Khala mbali yake

Sangakusiye.

Lengeza uthenga

Wamtenderewu.

Ufumu wa Khristu

Sudzatha konse.

(Onaninso Sal. 94:14; Miy. 3:5, 6; Aheb. 13:5.)