Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cifukwa Cake Tifunika Kupulumutsidwa

Cifukwa Cake Tifunika Kupulumutsidwa

“Munthu wobadwa kwa mkazi, Amakhala ndi moyo waufupi, wodzaza ndi masautso. Amaphuka ngati duwa n’kuthotholedwa. Amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalaponso.”—Yobu 14:1, 2.

Kuyambila kale, anthu akhala akulakalaka kukhala acinyamata kosatha ndiponso kukhala ndi umoyo wathanzi labwino. Komabe, n’zomvetsa cisoni kuti timafa. Yobu ananena mau ali pamwambawa zaka 3,000 zapitazo, ndipo akali oona mpaka masiku ano.

Munthu aliyense amalakalaka kukhala ndi moyo wosatha. Baibulo limatiuza kuti Mulungu anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Mlaliki 3:11) Popeza kuti zili conco, kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu wacikondi atipatse cinthu cimene sangathe kucikwanilitsa? Ngati yankho lanu ndi iyai, ndiye kuti mwayankha bwino. Mau a Mulungu amachula imfa kuti ndi mdani ndipo akutilonjeza kuti “idzaonongedwa.”—1 Akorinto 15:26.

Sitikukaikila zakuti imfa ndi mdani. Kulibe munthu wanzelu amene angaifune. Aliyense wa ife akaona coopsa amabisala kapena kuthawa. Tikadwala, timafunafuna njila zodzithandizila kuti tipole. Timacita zilizonse zimene tingathe kuti tipewe zinthu zimene zingacititse imfa.

Kodi pali cifukwa ciliconse cokhulupilila kuti mdani wakale ameneyu adzaonongedwa? Inde, cilipo. Yehova Mulungu, amene ndi Mlengi, sanalenge anthu n’colinga cakuti akhale ndi moyo kwa zaka zocepa cabe kenako n’kufa. Iye sanafune kuti anthu azifa. Mulungu anafuna kuti anthu akhale padziko lapansi kosatha ndipo iye adzakwanilitsa colinga cake.—Yesaya 55:11.

Nanga imfa idzaonongedwa motani? Kucokela kale, anthu akhala akuyesayesa kugonjetsa imfa, koma zimenezi zalepheleka. Masiku anonso anthu akhala akufufuza njila zothetsela imfa. Mwacitsanzo, Asayansi apanga mankhwala a katemela ndiponso mankhwala ogonjetsa matenda enaake. Iwo atulukilanso mmene magini a zamoyo amagwilila nchito. M’madela ambili anthu amakhalako ndi moyo wautali masiku ano kuposa zaka 100 zapitazo. Ngakhale ndi conco, io alephela kugonjetsa imfa. Monga mmene Baibulo limanenela, “zonse zimabwelela kufumbi.”—Mlaliki 3:20.

Uthenga wabwino ndi wakuti sitifunika kudalila anthu kuti ndi amene angathetse imfa. Yehova Mulungu wakonza kale za kutipululumutsa kwa mdani ameneyu imfa. Ndipo njila yaikulu imene adzagwilitsila nchito potipulumutsa ndi Yesu Kristu.