Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO|KODI MUNGAKONDE KUPHUNZILA BAIBULO?

Pulogalamu Yophunzila Baibulo ya Anthu Onse

Pulogalamu Yophunzila Baibulo ya Anthu Onse

Mboni za Yehova zimadziŵika bwino ndi nchito yao yolalikila. Koma kodi mumadziŵa kuti tilinso ndi pulogalamu yophunzitsa Baibulo padziko lonse?

Mu 2014, Mboni zoposa 8 miliyoni m’maiko 240 zinaphunzitsa Baibulo anthu pafupifupi 9.5 miliyoni mwezi uliwonse. * Ciŵelengelo ca amene timaphunzila nao Baibulo cimaposa ciŵelengelo ca anthu m’maiko ena 140 paokhapaokha.

Kuti zikwanitse kugwila nchito yophunzitsa imeneyi, Mboni za Yehova zimasindikiza Mabaibulo pafupifupi 1.5 biliyoni, mabuku, magazini, ndi zofalitsa zina zothandiza pophunzila Baibulo caka ciliconse m’zinenelo 700. Kusindikizidwa kwa zofalitsa m’zinenelo zosiyanasiyana, kwathandiza kuti anthu aphunzile Baibulo m’cinenelo cimene afuna.

MAYANKHO A MAFUNSO OFUNSIDWA KAŴILIKAŴILI OKHUDZA PULOGALAMU YATHU YOPHUNZITSA BAIBULO

Kodi phunzilo la Baibulo limacitika bwanji?

Timasankha nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo ndi kukambilana malemba ogwilizana ndi zimene tikuphunzila. Mwacitsanzo, Baibulo limayankha mafunso monga akuti: Kodi Mulungu ndani? Nanga ali ndi makhalidwe abwanji? Kodi ali ndi dzina? Nanga akhala kuti? Kodi n’zotheka kumuyandikila? Vuto ndi lakuti anthu sadziŵa mmene angapezele mayankho m’Baibulo.

Kuti tithandize anthu kupeza mayankho, timagwilitsila nchito buku lakuti, Zimene Baibo Imaphunzitsa. * Bukuli linakonzedwa kuti lithandize anthu kumvetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibulo. Lili ndi nkhani zokhudza Mulungu, Yesu Kristu, kuvutika kwa anthu, ciukililo, pemphelo, ndi zina zambili.

Ndi liti ndipo ndi kuti kumene kumacitikila phunzilo la Baibulo?

Mungacite phunzilo limeneli panthawi ndi malo amene mufuna.

Kodi phunzilo limatenga utali wotani?

Anthu ambili amapatula ola limodzi kapena angapo mlungu uliwonse kuti aphunzile Baibulo. Palibe nthawi yoikika ya kutalika kwa phunzilo, zimadalila mmene inuyo mwalinganizila zinthu. Ena amaphunzila mphindi 10 kapena 15 mlungu uliwonse.

Ndi ndalama zingati zimene mungalipile kuti muphunzile Baibulo?

Kosi imeneyi limodzi ndi mabuku ogwilitsila nchito pophunzila ndi zaulele. Izi ndi zogwilizana ndi zimene Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.”—Mateyu 10:8.

Kodi kosi yophunzila Baibulo imeneyi imatenga utali wotani?

Utali wa phunzilo limeneli ukudalila zimene inuyo mufuna kuphunzila. Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa Mceni-ceni lili ndi nkhani 19. Mungasankhe kuculuka kwa zimene mufuna kuphunzila.

Ngati ndavomela kuti ndiziphunzila Baibulo, kodi ndiyenela kukhala wa Mboni za Yehova?

Ai. Ife timazindikila kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene afuna kuti azikhulupilila. Conco, anthu amene aphunzila mfundo zoyambilila za m’Baibulo, angasankhe zimene afuna.

N’kuti kumene ndingadziŵile zambili?

Webusaiti ya jw.org ili ndi mfundo zolondola zokhudza zikhulupililo za Mboni za Yehova ndi zimene zimacita.

Ndingapemphe bwanji phunzilo la Baibulo?

  • Lembani fomu ya pa Intaneti yofunsila phunzilo la Baibulo pa www.jw.org.

  •  
  • Kambani ndi Mboni za Yehova za kwanuko.

^ par. 4 Timacita phunzilo limeneli ndi munthu aliyense payekha kapenanso m’tumagulu.

^ par. 9 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Makope oposa 230 miliyoni a buku limeneli asindikizidwa m’zinenelo zoposa 260.