Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUCEZA NA MUNTHU WINA

N’cifukwa Ciani Mulungu Amalola Kuti Anthufe Tizivutika?

N’cifukwa Ciani Mulungu Amalola Kuti Anthufe Tizivutika?

Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza mmene a Mboni za Yehova amacitila akamakambilana na anthu nkhani za m’Baibo. Tiyelekeze kuti mtsikana wina wa Mboni, dzina lake Alinafe, wafika pakhomo pa Mayi Phiri.

KODI MULUNGU AMAMVA BWANJI ANTHUFE TIKAMAVUTIKA?

Alinafe: Muli bwanji Mayi Phiri. Nasangalala kuti nakupezani.

Mayi Phiri: Nili bwino, inenso nasangalala kuti mwabwelanso.

Alinafe: Tsiku lija tinakambilana funso lakuti, ‘Kodi Mulungu amamva cisoni tikamavutika?’ a Munaniuza kuti mwakhala mukudzifunsa funso limeneli kwa nthawi yaitali, maka-maka kuyambila pamene amayi anu anavulala pa ngozi ya galimoto. Koma kodi mayi anu akumvelako bwanji?

Mayi Phiri: Ali bwino conco. Poti amangoti lelo aukeko bwino, mawa adwale. Koma lelo kasako aukako bwino.

Alinafe: Nasangalala kuti akumvelako bwino. Nikudziŵa kuti kudwazika matenda n’kovuta, komabe mukuyesetsa kuti musamangokhala wokhumudwa cifukwa ca zimenezi.

Mayi Phiri: N’kovutadi. Moti nthawi zina nimadzifunsa kuti, akhala conco mpaka liti?

Alinafe: Ni mmene aliyense angamvele. Tsiku lija, ndinati lelo tidzakambilana funso lakuti, ‘Popeza Mulungu ali na mphamvu zothetsela mavuto, n’cifukwa ciani walola kuti mavutowa azicitikabe?’

Mayi Phiri: Nakumbukiladi.

Alinafe: Tisanakambilane yankho la funso limeneli, tiyeni tikumbutsane coyamba zimene tinakambilana tsiku lija.

Mayi Phiri: Cabwino.

Alinafe: Coyamba, tinaona kuti m’Baibo muli nkhani ya mtumiki wina wa Mulungu amene anali kudabwa kuti n’cifukwa ciani Mulungu amalola kuti anthu azivutika. Koma Mulungu sanam’dzudzule cifukwa ca zimenezi komanso sanamuuze kuti alibe cikhulupililo.

Mayi Phiri: Nakumbukiladi kuti tinakambilana zimenezi.

Alinafe: Tinaphunzilanso kuti Mulungu sasangalala akamationa tikuvutika. Mwacitsanzo, Baibo imanena kuti anthu ake akamavutika, ‘iyenso anali kuvutika.’ b Kodi si zolimbikitsa kudziŵa kuti Mulungu amamva cisoni tikamavutika?

Mayi Phiri: N’zolimbikitsadi.

Alinafe: Pomalizila, tinagwilizana pa mfundo yoti, popeza Mlengi ali na mphamvu zambili, atafuna angathe kuthetsa mavuto amene ali padzikoli.

Mayi Phiri: N’zoonadi. Koma ine nikudabwa kuti n’cifukwa ciani Mulungu amalola kuti zoipa zizicitikabe, pomwe iyeyo ali na mphamvu zoti akhoza kuzithetsa?

NDANI ANANENA ZOONA?

Alinafe: Kuti tipeze yankho la funso lanuli, tiyeni tiyambe n’kukambilana nkhani imene ili koyambilila kwa buku la Genesis. Kodi munamvapo za Adamu na Hava komanso za cipatso cimene Mulungu anawauza kuti asadye?

Mayi Phiri: Ee, n’naphunzilapo nkhani imeneyi ku Sande sukulu. Mulungu anawauza kuti asadye zipatso za mtengo winawake koma iwo sanamvele ndipo anadya zipatso za mtengowo.

Alinafe: Mwafotokoza bwino. Ndiye tiyeni tione zimene zinacititsa kuti Adamu na Hava adye zipatso za mtengowo, komwe kunali kucimwila Mulungu. Zimene zinacitikazo zitithandiza kudziŵa kuti n’cifukwa ciani anthufe timavutika. Kodi mungaŵelenge lemba la Genesis 3, vesi 1 mpaka 5?

Mayi Phiri: Ee nikhoza kuŵelenga. “Tsopano njoka inali yocenjela kwambili kuposa nyama zonse zakuchile zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?’ Pamenepo mkaziyo anayankha njokayo kuti: ‘Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, “Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.”’ Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: ‘Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziŵa kuti tsiku limene mudzadye cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.’”

Alinafe: Zikomo, mwaŵelenga bwino. Tiyeni tikambilane bwino-bwino mavesi amenewa. Coyamba, onani kuti njoka inalankhula na Hava. Buku la m’Baibo la Chivumbulutso, limasonyeza kuti Satana Mdyerekezi ni amene analankhula na Hava kudzela mwa njokayo. c Ndipo anafunsa Hava za lamulo limene Mulungu anawapatsa. Kodi mwaona cilango cimene Mulungu ananena kuti Adamu na Hava adzalandila akadzadya zipatso za mtengowo?

Mayi Phiri: Ee, anawauza kuti adzafa.

Alinafe: Zoona zimenezo. Taonaninso zimene Satana ananena potsutsa zimene Mulungu ananena. Iye anati: “Kufa simudzafa ayi.” Apatu Satana anali kunena kuti Mulungu ni wabodza.

Mayi Phiri: N’nali nisanamvepo zimenezi.

Alinafe: Ponena kuti Mulungu ni wabodza, Satana anayambitsa nkhani imene inafunika nthawi kuti ithetsedwe. Kodi mukudziŵa cifukwa cake zili conco?

Mayi Phiri: Ayi, sinikudziŵa.

Alinafe: N’takufunsani funso ili, kodi mungacite ciani munthu wina atanena kuti ni wamphamvu kuposa inuyo?

Mayi Phiri: Nikhonza kumuuza kuti ticite cinacake kuti wamphamvu adziŵike.

Alinafe: Zoona. Mwina mungapeze cinthu colemela kwambili kuti muone amene angakwanitse kucinyamula. Conco sizingavute kuti anthu adziŵe kuti, pakati pa inuyo na munthuyo, wamphamvu ndani.

Mayi Phiri: Tsopano nayamba kumvetsa.

Alinafe: Koma bwanji zitakhala kuti munthu wina akunena kuti iyeyo ni wacilungamo kuposa inuyo? Mwina zingakhale zovuta kuti anthu adziŵe mwamsanga kuti wacilungamo ndani, si conco?

Mayi Phiri: Zingakhaledi zovuta.

Alinafe: N’zoona, cifukwa pamafunika nthawi kuti anthu azindikile munthu wacilungamo.

Mayi Phiri: Mukutanthauza ciani?

Alinafe: Njila yabwino yothetsela nkhaniyi ingakhale kulola kuti padutse nthawi kuti anthu aone zocita za inuyo komanso za munthu winayo, n’kuzindikila kuti wacilungamo ndani.

Mayi Phiri: Zimenezidi n’zomveka.

Alinafe: Ndiyeno tiyeni tionenso nkhani ya m’buku la Genesis ija. Kodi Satana ananena kuti iyeyo ali na mphamvu zambili kuposa Mulungu?

Mayi Phiri: Ayi.

Alinafe: Mwayankha bwino. Akanakhala kuti ananena zimenezo, nthawi yomweyo Mulungu akanatha kucita zinthu zosonyeza kuti iye ni wamphamvu kuposa Satana. Koma Satana ananena kuti iyeyo ni wacilungamo kuposa Mulungu. Tingati iye anauza Hava kuti, ‘Mulungu anakunamizani, ine ni amene nikukuuzani zoona.’

Mayi Phiri: Komadi eti!

Alinafe: Conco, mwanzelu zake, Mulungu anadziŵa kuti njila yabwino yothetsela nkhani imeneyi n’kulola kuti papite nthawi yokwanila kuti cilungamo cidziŵike. Anadziŵa kuti pakapita nthawi, zidzadziŵika kuti ananena zoona ndani, nanga wabodza ndani.

PAMENE PANAGONA NKHANI

Mayi Phiri: Koma pamene Hava anafa, sindiye kuti zinadziŵika kuti Mulungu ni amene ananena zoona?

Alinafe: Tingati zinadziŵikadi. Komabe nkhaniyi inali isanathe. Taonaninso zimene vesi 5 likunena. Kodi ni zinthu zinanso ziti zimene Satana anauza Hava?

Mayi Phiri: Anamuuza kuti akadya zipatso za mtengo woletsedwa, maso ake adzatseguka.

Alinafe: Zoona, ndipo anamuuzanso kuti ‘adzafanana na Mulungu ndipo adzadziŵa zabwino na zoipa.’ Conco, Satana ananena kuti Mulungu anabisila anthu zinthu zinazake zabwino.

Mayi Phiri: N’zoonadi.

Alinafe: Nkhani imeneyinso ni yaikulu.

Mayi Phiri: Mukutanthauza ciani?

Alinafe: Satana anatanthauza kuti Hava, komanso anthu ena onse, angakhale mosangalala popanda kulamulidwa na Mulungu. Apanso Yehova anaona kuti njila yabwino yothetsela nkhaniyi, n’kumulola Satana kuti asonyeze ngati zimene ananenazo zinali zoona. Conco Mulungu analola kuti Satana alamulile dzikoli kwa nthawi. N’cifukwa cake padzikoli pali mavuto ambili poti Satana, osati Mulungu, ni amene akulamulila dzikoli.  dKomabe pali nkhani yabwino.

Mayi Phiri: Nkhani yabwino yotani?

Alinafe: Baibo imasonyeza kuti Yehova sasangalala anthufe tikamavutika. Mwacitsanzo, taonani zimene Mfumu Davide inalemba pa Salimo 31:7. Davide anakumana na mavuto ambili, koma tiyeni tione zimene anauza Yehova m’pemphelo lake. Kodi mungaŵelenge vesi limeneli?

Mayi Phiri: Cabwino. Lembali likuti: “Ndidzakondwela ndi kusangalala cifukwa ca kukoma mtima kwanu kosatha, pakuti mwaona kusautsika kwanga. Mwadziŵa zowawa zimene zandigwela.”

Alinafe: Zikomo kwambili. Conco ngakhale kuti Davide anali kukumana na mavuto, iye anali kulimba mtima cifukwa codziŵa kuti Yehova akudziŵa mavuto ake onse. Kodi si zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amadziŵa mavuto athu onse, ngakhale amene anthu ena sangawamvetsetse?

Mayi Phiri: Koma ndiye n’zolimbikitsadi.

Alinafe: Cinanso n’cakuti Mulungu sadzalola kuti mavuto amene akucitika padzikoli apitilile mpaka kale-kale. Baibo imaphunzitsa kuti posacedwapa, Satana sadzalamulilanso dzikoli cifukwa Mulungu adzamucotsa. Komanso Mulungu adzakonza zinthu zoipa zonse zimene Satana wabweletsa padzikoli, kuphatikizapo mavuto amene inuyo na mayi anu mukukumana nawo. Bwanji nidzabwelenso mlungu wamawa kuti nidzakusonyezeni zimene Mulungu adzacite posacedwapa pocotsa mavuto onse padzikoli? e

Mayi Phiri: Ee mudzabwele mudzanipeza.

Kodi pali nkhani inayake ya m’Baibo imene simumaimvetsa? Kapena mumafuna mutadziŵa zimene a Mboni za Yehova amakhulupilila? Ngati ni conco, funsani a Mboni za Yehova ndipo adzasangalala kwambili kukambilana nanu.

a Ŵelengani nkhani yakuti “Kuceza Ni Munthu Wina—Kodi Mulungu Amamva Cisoni Tikamavutika?” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2013.

b Onani Yesaya 63:9.

c Onani Chivumbulutso 12:9.

d Onani Yohane 12:31 na 1 Yohane 5:19.

e Kuti mudziŵe zambili, ŵelenganimutu 9 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa na Mboni za Yehova.