Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI IMFA NDI MAPETO A ZONSE?

Imfa Si Mapeto a Zonse

Imfa Si Mapeto a Zonse

Betaniya unali mudzi waung’ono umene unali pa mtunda wa makilomita atatu kucokela ku Yerusalemu. (Yohane 11:18) Kutatsala milungu yocepa Yesu asanamwalile, m’mudzi umenewu munacitika cinthu cina comvetsa cisoni. Lazaro, mmodzi wa mabwenzi apamtima a Yesu, mosayembekezeka anadwala kwambili ndi kumwalila.

Yesu atamva uthenga umenewu, anauza ophunzila ake kuti Lazaro anali mtulo ndipo anali kufuna kupita kuti akam’dzutse. (Yohane 11:11) Koma ophunzila a Yesu sanamvetsetse zimene anatanthauza, conco Yesu anawauza momveka bwino kuti: “Lazaro wamwalila.”—Yohane 11:14.

Patapita masiku anai Lazaro ali m’manda, Yesu anafika ku Betaniya kuti akatonthoze Marita, mlongosi wa womwalilayo. Marita anati: “Mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalila.” (Yohane 11:17, 21) Yesu anayankha kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupilila mwa ine, ngakhale amwalile, adzakhalanso ndi moyo.”—Yohane 11:25.

“Lazaro, tuluka!”

Kuti aonetse kuti mau amenewo analidi oona, Yesu anayandikila manda ndi kufuula kuti: “Lazaro, tuluka!” (Yohane 11:43) Womwalilayo anatuluka, ndipo anthu amene anali kuonelela anadabwa kwambili.

Yesu anali ataukitsapo anthu aŵili m’mbuyomo panthawi zosiyana. Panthawi ina, anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo. Yesu asanaukitse mtsikanayu, ananenanso kuti mwanayo anali m’tulo.—Luka 8:52.

Onani kuti ponena za imfa ya onse aŵili, Lazaro ndi mwana wamkazi wa Yairo, Yesu anayelekezela imfa ndi tulo. Kumeneku ndi kuyelekezela kwabwino. N’cifukwa ciani tikutelo? Tulo ndi mkhalidwe wosadziŵa ciliconse ndipo munthu amene ali mu mkhalidwe umenewu samamva kupweteka. (Mlaliki 9:5; onani bokosi lakuti,  “Imfa Ili Ngati Tulo Tofa Nato.”) Ophunzila oyambilila a Yesu anamvetsetsa zimene zimacitika munthu akamwalila. Buku lina limati, “Ophunzila a Yesu anali kuona kuti imfa ndi tulo, ndipo manda ndi malo opumulila . .  anthu amene anafa ali ndi cikhulupililo.” aEncyclopedia of Religion and Ethics.

N’zotonthoza kwambili kudziŵa kuti akufa ali m’tulo m’manda ndipo sakuvutika. Conco, tadziŵa zimene zimacitika tikamwalila ndipo sitifunikilanso kucita mantha.

“MUNTHU AKAFA, KODI ANGAKHALENSO NDI MOYO?”

Ngakhale kuti timasangalala kugona tulo twabwino, palibe amene angafune kugona osadzukanso. Kodi tili ndi ciyembekezo cotani cakuti akufa amene ali gone m’manda adzakhalanso ndi moyo monga mmene Lazaro ndi mwana wamkazi wa Yairo anacitila?

Yobu anafunsa funso lofanana ndi limeneli pamene anaona kuti ali pafupi kufa. Iye anati: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?”—Yobu 14:14.

Polankhula ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Yobu anadziyankhila funso lake kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka nchito ya manja anu.” (Yobu 14:15) Yobu anali kudziŵa kuti ngakhale afe, Yehova adzalaka-laka kuukitsa mtumiki Wake wokhulupilika. Kodi Yobu anali kungofuna zinthu zosatheka? Iyai.

Kuukitsa anthu akufa kumene Yesu anacita kunali umboni woonekelatu wakuti Mulungu anam’patsa mphamvu zogonjetsa imfa. Ndipo Baibo imanena kuti Yesu tsopano ali ndi “makiyi a imfa.” (Chivumbulutso 1:18) Conco Yesu adzatsegula zitseko za kumanda. Monga mmene analili ndi mphamvu zoukitsa Lazaro, Yesu alinso ndi mphamvu zoukitsa anthu mtsogolo.

Mobweleza-bweleza, Baibo imanena za lonjezo lakuti akufa adzauka. Mngelo analimbikitsa mneneli Danieli kuti: “Udzapuma. Koma udzauka kuti ulandile gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Danieli 12:13) Yesu anauza Asaduki, atsogoleli a Ayuda amene anali kukana kuti akufa adzauka, kuti: “Mukulakwitsa cifukwa simudziŵa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.” (Mateyu 22:23, 29) Mtumwi Paulo anati: “Ine ndili ndi ciyembekezo mwa Mulungu. . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.

KODI AKUFA ADZAUKA LITI?

Kodi kuuka kwa olungama ndi osalungama kudzacitika liti? Mngelo anauza Danieli wolungamayo kuti adzauka “pa mapeto a masikuwo.” Marita nayenso anali kukhulupilila kuti mlongo wake, Lazaro, “adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.”—Yohane 11:24.

Baibo imagwilizanitsa ‘tsiku lomaliza’ ndi ulamulilo wa Ufumu wa Kristu. Paulo analemba kuti: “Pakuti [Kristu] ayenela kulamulila monga mfumu kufikila Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Imfa nayonso, monga mdani womalizila, idzaonongedwa.” (1 Akorinto 15:25, 26) Ici ndi cifukwa cabwino kwambili cimene tiyenela kupemphelela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele ndi kuti cifunilo ca Mulungu cicitike padziko lapansi. b

Yobu anali kudziŵa kuti Mulungu amafuna kuukitsa akufa. Zimenezi zikadzacitika, imfa idzaonongedwa kothelatu. Ndipo sipadzakhalanso munthu wofunsa kuti, ‘Kodi imfa ndi mapeto a zonse?’

a Liu la Cigiriki limene linatembenuzidwa kuti “manda” limatanthauza “malo ogonako.”

b Kuti mudziŵe zambili za Ufumu wa Mulungu, onani nkhani 8 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Cithunzi papeji 6]