Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBO IMASINTHA ANTHU

“N’nayamba Kuganizila Kwambili za Moyo Wanga”

“N’nayamba Kuganizila Kwambili za Moyo Wanga”
  • CAKA COBADWA: 1941

  • DZIKO: AUSTRALIA

  • POYAMBA: N’NALI KUKOKA FODYA NA KUMWA MOŴA MWAUCIDAKWA

KALE LANGA:

N’nakulila ku Warialda, tauni yaing’ono yomwe ili ku New South Wales. Anthu a ku Warialda amaweta nkhosa, ng’ombe komanso amalima tiligu na mbewu zina. Tauniyi ni yabata cifukwa anthu sakonda kucita zaciwawa.

M’banja mwathu tinalimo ana 10, ndipo ineyo n’nali woyamba. Nili na zaka 13, n’nayamba kugwila nchito kuti nizithandiza kusamalila banja lathu. Cifukwa cakuti sininaphunzile kwambili sukulu n’nali kugwila nchito pa famu. Nili na zaka 15, n’nayamba kugwila nchito yosamalila mahachi.

Kugwila nchito pa famu kunali na ubwino komanso mavuto ake. Ubwino wake unali wakuti nchitoyo inali kunisangalatsa cifukwa n’nali kukonda kugona kuchile, kuona nyenyezi na mwezi usiku komanso n’nali kusangalala kumva fungo la maluwa onunkhila a m’chile. N’kamaona zimenezi n’nali kuganiza zoti pali winawake amene analenga zinthu zonsezi. Koma kugwila nchitoyi kunanipangitsa kuti nitengele makhalidwe ena oipa. Nthawi zambili anthu amene n’nali kugwila nawo nchito anali kukonda kutukwana komanso kukoka fodya. Zimenezi zinacititsa kuti nitengele makhalidwe amenewa.

N’takwanitsa zaka 18, n’nasamukila ku Sydney. N’nali kufuna kulowa usilikali koma zinakanika cifukwa cakuti sininaphunzile kwambili sukulu. N’napeza nchito ina ndipo n’nakhala ku Sydney caka cimodzi. Nthawi imeneyi ni imene ninakumana koyamba na Mboni za Yehova. Ananiitanila ku misonkhano yawo ndipo nitapita ninazindikila kuti amaphunzitsa zoona.

Komabe patapita nthawi, n’naganiza zokayambilanso nchito yosamalila mahachi. N’nasamukila ku tauni ya Goondiwindi, ku Queensland. N’tafika kumeneko n’napeza nchito koma n’nayamba kumwa moŵa.

N’nakwatila ndipo ninakhala na ana aamuna aŵili. Anawo atabadwa n’nayamba kuganizila kwambili za moyo wanga. N’nakumbukila zimene ninamva pamsonkhano wa Mboni za Yehova ku Sydney, ndipo n’naona kuti nikufunika kusintha zinthu zina pa moyo wanga.

N’napeza magazini ya Nsanja ya Mlonda yomwe inali na adilesi ya ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Australia. N’natumiza kalata yopempha kuti munthu wina adzanithandize ndipo pasanapite nthawi yaitali, munthu wina wa Mboni anabwela n’kuyamba kuniphunzitsa Baibo. Munthuyo anali wacifundo komanso wacikondi.

MMENE BAIBO INASINTHILA MOYO WANGA:

N’tayamba kuphunzila Baibo, n’naona kuti nikufunika kusintha zinthu zambili pa moyo wanga. Lemba limene linanikhudza kwambili ni la 2 Akorinto 7:1. Lembali limatilimbikitsa kuti: “Tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi.”

N’naganiza zosiya kukoka fodya na kumwa moŵa kwambili. Zinali zovuta kwambili kusintha cifukwa n’nali nitazolowela kucita zimenezi kwa nthawi yaitali. Koma n’nali kufunitsitsa kucita zinthu zokondweletsa Mulungu. Mfundo imene inanithandiza kwambili ni imene imapezeka pa lemba la Aroma 12:2, yomwe imati: “Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” N’nazindikila kuti ngati nikufuna kusintha makhalidwe anga oipa, nikufunika niyambe kusintha mmene n’maganizila, n’kuyamba kuona makhalidwe oipawo mmene Mulungu amawaonela. Zimenezi zinanithandiza kuti nisiye kukoka fodya komanso kumwa moŵa kwambili.

“N’nazindikila kuti ngati nikufuna kusintha makhalidwe anga oipa, nikufunika niyambe kusintha mmene nimaganizila”

Koma ninavutika kwambili kuti nisiye kutukwana. N’nali kudziŵa ndithu malangizo a m’Baibo omwe ali pa Aefeso 4:29, omwe amati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.” Komabe sininasiyiletu kutukwana. Kenako ninaona kuti kuganizila kwambili lemba la Yesaya 40:26 kunganithandize. Lembali limanena za nyenyezi zakumwamba. Limati: “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo? Ndi amene akutsogolela gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi ciŵelengelo cake, ndipo amaziitana pochula iliyonse dzina lake. Cifukwa ca kuculuka kwa mphamvu zake zoopsa, ndiponso cifukwa cakuti ali ndi mphamvu zambili zocitila zinthu, palibe imene imasowa.” N’nayamba kuganiza kuti ngati Mulungu ali ni mphamvu zomwe analengela cilengedwe conse, sangalephele kunipatsa mphamvu zomwe zinganithandize kuti nizicita zinthu zomukondweletsa. N’nali kuyesetsa kucita khama komanso kupemphela ndipo kenako ninasiyilatu kutukwana.

PHINDU LIMENE NAPEZA:

Poyamba sininali kukonda kuceza na anthu cifukwa kufamu kumene n’nali kugwila nchito kuja kunali anthu ocepa. Koma cifukwa ca zimene naphunzila ku misonkhano ya Mboni za Yehova, nimatha kuceza na anthu. Zimenezi zanithandizanso kuti niziuza anthu ena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 6:9, 10; 24:14.

Tsopano nakhala nikutumikila monga mkulu mu mpingo kwa zaka zingapo. Nimaona kuti ni mwayi waukulu kuthandiza Akhristu anzanga m’njila zosiyana-siyana. Koma phindu lalikulu limene napeza ni lakuti panopa nikutumikila Yehova limodzi na mkazi wanga komanso ana anga.

Nimathokoza kwambili Yehova cifukwa coniphunzitsa, ngakhale kuti sininaphunzile kwambili sukulu. (Yesaya 54:13) Nimaona kuti mawu a pa Miyambo 10:22, ni oona. Mawuwa amati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeletsa.” Ineyo na banja langa tikufunitsitsa kupitilizabe kuphunzitsidwa na Yehova komanso kumutumikila mpaka kale-kale.