Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Amaona Nchito Yanu

Yehova Amaona Nchito Yanu

BEZALELI ndi Oholiabu anali kudziŵa nchito yomanga. Pamene anali akapolo ku Iguputo anapanga nchelwa zambili moti sanafune kukumbukila za nchitoyo cifukwa inali yaukapolo. Koma nthawi ya ukapolo inali itapita, ndipo anakhala amisili aluso pamene Yehova anawasankha kuti atsogolele pa nchito yomanga cihema. (Eks. 31:1-11) Ngakhale n’conco, ndi anthu ocepa cabe amene anaona nchito yapamwamba imene Bezaleli ndi Oholiabu anagwila. Koma kodi anakhumudwa podziŵa kuti ndi anthu ocepa amene anaona nchito yao? Ndani anafunika kuona nchito yao? Nanga ndani afunika kuona nchito yanu?

NCHITO YAPAMWAMBA IMENE INAONEDWA NDI ANTHU OCEPA

Zinthu zina zokongoletsela pa cihema zinali zopangidwa mwaluso. Mwacitsanzo, akelubi a golide amene anali pamwamba pa likasa la pangano anapangidwa mwaluso kwambili. Mtumwi Paulo ananena kuti anali “aulemelelo.” (Aheb. 9:5) Akelubi amenewo anapangidwa ndi golide ndipo anali okongola kwambili.—Eks. 37:7-9.

Zinthu zimene Bezaleli ndi Oholiabu anapanga zitapezeka masiku ano, zingaikidwe m’malo apamwamba kwambili osungilako zinthu zakale, ndipo anthu ambili angacite nazo cidwi kwambili. Koma kodi ndi anthu angati amene anaziona panthawiyo? Akelubi anaikidwa m’Malo Oyela Koposa ndipo ndi mkulu wa ansembe yekha amene anali kuwaona. Iye anali kuwaona kamodzi pa caka akaloŵa m’malo oyelawo pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo. (Aheb. 9:6, 7) Conco, ndi anthu ocepa cabe amene anaona akelubiwo.

MUZIKHUTILA NDI NCHITO YANU POPANDA KUFUNA KUCHUKA

Mukanakhala Bezaleli kapena Oholiabu ndipo mwagwila mwakhama nchito ya luso imeneyo koma ndi anthu ocepa amene akuidziŵa, kodi mukanamva bwanji? Masiku ano, anthu ambili amakhutila ndi nchito imene agwila kokha ngati anzao awatamanda cifukwa ca nchitoyo. Koma atumiki a Yehova ndi osiyanako. Monga Bezaleli ndi Oholiabu, timakhala okhutila kucita cifunilo ca Yehova podziŵa kuti iye akusangalala ndi nchito yathu.

Pamene Yesu anali padziko lapansi, atsogoleli azipembedzo anali kukonda kupeleka mapemphelo odzionetsela. Koma Yesu anawalangiza kuti ayenela kupemphela moona mtima osati ndi colinga cakuti ena awatamande. Kodi pali ubwino wotani? Iye anati: “Ukatelo Atate wako amene amaona kucokela kosaonekako adzakubwezela.” (Mat. 6:5, 6) N’zoonekelatu kuti cofunika kwambili si mmene anthu amaonela mapemphelo athu koma mmene Yehova amawaonela. Mapemphelo athu angakhale opanda phindu ngati Yehova sanawavomeleze. Ndi mmenenso zilili ndi nchito iliyonse imene timagwila pomutumikila. Tisadele nkhawa ngati anthu sanayamikile nchito yathu. Cofunika kwambili n’cakuti nchitoyo imasangalatsa Yehova amene “amaona kucokela kosaonekako.”

Nchito yomanga cihema itatha, “mtambo unayamba kuphimba cihema cokumanako, ndipo ulemelelo wa Yehova unadzaza m’cihemaco.” (Eks. 40:34) Cimeneci cinali cizindikilo cakuti Yehova anasangalala ndi nchitoyo. Muganiza kuti Bezaleli ndi Oholiabu anamva bwanji pa nthawiyo? Ngakhale kuti maina ao sanalembedwe pa zinthu zimene anapanga, ayenela kuti anakhutila podziŵa kuti Mulungu wadalitsa nchitoyo. (Miy. 10:22) Patapita zaka zambili, io ayenela kuti anali kusangalala kuona kuti zinthu zimene anapanga zikugwilabe nchito mu utumiki wa Yehova. Ndipo akadzaukitsidwa m’dziko latsopano, Bezaleli ndi Oholiabu adzasangalala kwambili kudziŵa kuti cihema cinagwilitsidwa nchito pa kulambila koona kwa zaka 500.

Ngakhale kuti anthu ena sangaone nchito imene mumagwila, Yehova amaona

M’gulu la Yehova masiku ano muli abale ndi alongo amene amakonza mavidiyo, kujambula zithunzi, kuimba nyimbo, kumasulila mabuku, ndi kulemba nkhani. Onsewa maina ao sadziŵika. M’mipingo yoposa 110,000 padziko lonse mukucitikanso nchito imene anthu ena sadziŵa zolowetsedwamo. Mwacitsanzo, ndani amaona nchito yoonkhetsa ndalama ndi kudzaza mapepala a maakaunti imene mtumiki wa maakaunti amacita mwezi ulionse? Ndani amaona nchito imene mlembi amakhala nayo posonkhanitsa malipoti a utumiki wa kumunda? Nthawi zina m’bale kapena mlongo akakonza zimene zaonongeka pa Nyumba ya Ufumu palibe amene amadziŵa.

Kumapeto kwa moyo wao, Bezaleli ndi Oholiabu sanalandile mendulo, cikho, kapena zinthu zina powayamikila kaamba ka zinthu zimene anapanga ndi kumanga mwaluso. Koma anapeza cinthu camtengo wapatali comwe ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’zodziŵikilatu kuti Yehova anaona nchito imene anagwila. Tiyeni tiyesetse kutsatila citsanzo cao ca kudzicepetsa ndi kutumikila Mulungu modzipeleka.