NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA July 2015

M’magazini ino muli nkhani zophunzila kuyambila mlungu wa August 31 mpaka September 27, 2015.

Anadzipeleka Mofunitsitsa ku Russia

Ŵelengani zambili zokhuza Akristu a pabanja ndiponso amene sali pabanja amene anasamukila ku malo osoŵa m’dziko la Russia. Iwo anaphunzila kudalila kwambili Yehova

Thandizani Kukongoletsa Paladaiso Wauzimu

Kodi mau akuti paladaiso wauzimu ndi akuti kacisi wauzimu ndi ofanana? Ndi “paladaiso” uti amene Paulo anaona pamene “anakwatulidwila kumwamba kwacitatu”?

Kutumikila Yehova ‘m’Masiku Oipa’

Mungaonetse bwanji cikhulupililo colimba ndi kupitilizabe kutumikila Yehova? Ganizilani za atumiki a Mulungu akale amene anamutumikila ndi cimwemwe.

“Cipulumutso Canu Cikuyandikila”

Ndi uthenga wotani umene udzalalikidwa cisautso cacikulu cikadzayamba? N’ciani cidzacitikila odzozedwa pa nthawiyo?

Yehova Amaona Nchito Yanu

Citsanzo ca Bezaleli ndi Oholiabu cingatithandize kuyamikila coonadi cimeneci: Yehova amaona nchito yanu, ngakhale kuti kulibe amene angaone.

Khalanibe Okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu

Kodi Akristu angadziphunzitse bwanji kukhala okhulupilika kwa Yehova ndi ku Ufumu wake?

Awa Ndi Malo Athu Olambilila

Kodi tingaonetse bwanji ulemu pa malo athu olambilila? Kodi ndalama zomangila ndi kukonza Nyumba za Ufumu zimacokela kuti?

KODI MUDZIŴA?

Baibulo limafotokoza kuti madela ena a Dziko Lolonjezedwa anali ndi nkhalango zoŵilila. Popeza kuti masiku ano kulibe nkhalango zoŵilila ngati za m’nthawi ya Isiraeli, kodi zimene Baibulo limanena n’zoona?