Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 8

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

Musaleke Kutsatila Citsogozo ca Yehova

Musaleke Kutsatila Citsogozo ca Yehova

“Ine Yehova. . . amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.”YES. 48:17.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Nkhani ino itithandiza kuona mmene Yehova amatsogolela anthu ake masiku ano, komanso madalitso amene timasangalala nawo tikatsatila citsogozo cake.

1. Fotokozani citsanzo coonetsa kufunika kotsatila mtsogoleli wathu Yehova.

 YELEKEZANI kuti mwasocela m’nkhalango. Moyo wanu uli pa ciopsezo cifukwa m’nkhalangoyo muli nyama zolusa, tudoyo topatsa matenda, zomela za poizoni, komanso maenje obisika. Kunena zoona, mungayamikile ngako kutabwela wokulondolelani njila amene aidziŵa bwino nkhalangoyo, wodziŵanso kuli zoopsazo, amene angakuthandizeni mozipewela! Dzikoli ili ngati nkhalango yoopsa imeneyo. Ni lodzala na zinthu zoopsa zimene zimaika moyo wathu wauzimu pa ciopsezo. Koma tili na Wotilondolela njila wabwino kopambana—Yehova. Amatipulumutsa ku zinthu zoopsa na kutitsogolela kumene tikupita—ku moyo wosatha m’dziko latsopano.

2. Kodi Yehova amatitsogolela motani?

2 Kodi Yehova amatilondelela njila motani? Amatelo maka-maka kupitila m’Baibo. Komabe, amaseŵenzetsanso anthu omuimilako. Mwacitsanzo, amaseŵenzetsa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” amene amatipatsa cakudya cauzimu cotithandiza kupanga zisankho zanzelu. (Mat. 24:45) Yehova amagwilitsanso nchito amuna ena ofikapo potitsogolela. Mwacitsanzo, oyang’anila madela, komanso akulu amapeleka cilimbikitso na malangizo otithandiza kupilila pa nthawi zovuta. Timayamikila zedi citsogozo codalilika comwe timalandila m’nthawi ino ya masiku otsiliza. Citsogozo cimeneco cimatithandiza kukhalabe ovomelezeka kwa Yehova na kupitiliza kuyendabe pa njila ya ku moyo.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Ngakhale n’telo, nthawi zina cingakhale covuta kutsatila citsogozo ca Yehova maka-maka cikapelekedwa na anthu opanda ungwilo. Cifukwa ciyani? Nthawi zina uphunguwo sungagwilizane na zimene tikufuna. Kapena tingaone kuti citsogozoco n’cosathandiza, ndipo n’cosacokela kwa Yehova. Pa nthawi zotelezi tifunika kulimbitsa cidalilo kwambili cakuti Yehova ndiye amatsogolela anthu ake, ndipo kutsatila citsogozo cake kumabweletsa madalitso. Kuti tilimbikitse cidalilo cathu, m’nkhani ino tikambilane (1) mmene Yehova anatsogolela anthu ake m’nthawi za anthu ochulidwa m’Baibo, (2) mmene amatitsogolela masiku ano, ndiponso (3) mmene timapindulila tikapitiliza kutsatila citsogozo cake.

Kucokela kale mpaka masiku ano, Yehova wakhala akugwilitsa nchito anthu omuimilako kutsogolela anthu ake (Onani ndime 3)


MMENE YEHOVA ANATSOGOLELA AISIRAELI

4-5. Kodi Yehova anaonetsa motani kuti anali kugwilitsa nchito Mose potsogolela Aisiraeli? (Onani cithunzi pa cikuto.)

4 Yehova anasankha Mose kuti atsogolele Aisiraeli kutuluka mu Iguputo. Ndipo anawapatsa umboni woonekelatu kuti anali kuwatsogolela kupitila mwa Mose. Mwacitsanzo, Iye anawaikila cipilala ca mtambo masana, komanso moto usiku. (Eks. 13:21) Mose anatsatila mtambowo umene unamutsogolela pamodzi na Aisiraeli onse ku Nyanja Yofiila. Anthuwo anacita mantha pamene anafika ku Nyanja Yofiila, ndipo asilikali aciiguputo anali kuwalondola m’mbuyo mwawo. Iwo anaona kuti Mose analakwitsa kuwatsogolela ku Nyanja Yofiila. Koma sanalakwitse ayi. Yehova ndiye anatsogolela anthuwo kumeneko kupyolela mwa Mose. (Eks. 14:2) Kenako Mulungu anawapulumutsa m’njila yodabwitsa zedi.—Eks. 14:​26-28.

Mose anadalila cipilala ca mtambo potsogolela anthu a Mulungu m’cipululu (Onani ndime 4-5)


5 Kwa zaka 40 zotsatila, Mose anadalilabe cipilala ca mtambo potsogolela anthu a Mulungu m’cipululu. a Kwa kanthawi, Yehova anaika cipilala ca mtambo pamwamba pa hema wa Mose pomwe Aisiraeli onse anatha kuciona. (Eks. 33:​7, 9, 10) Yehova anali kulankhula na Mose kupitila mu mtambowo, kenako iye anali kuuza anthu onse malangizo amenewo. (Sal. 99:7) Aisiraeli anali na umboni wokwanila wakuti Yehova anali kugwilitsa nchito Mose kuwatsogolela.

Mose komanso womuloŵa m’malo Yoswa (Onani ndime 5, 7)


6. Kodi Aisiraeli anaciona motani citsogozo ca Yehova? (Numeri 14:​2, 10, 11)

6 N’zacisoni kuti Aisiraeli ambili anakana umboni woonekelatu wakuti Yehova anali kuseŵenzetsa Mose monga womuimilako. (Ŵelengani Numeri 14:​2, 10, 11.) Mobweleza-bweleza, iwo anakana zakuti Yehova ndiye anali kugwilitsa nchito Mose. Zotulukapo zake zinali zakuti m’badwo umenewo sunaloledwe kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 14:30.

7. Chulani zitsanzo za amene anatsatila citsogozo ca Yehova. (Numeri 14:24) (Onaninso cithunzi.)

7 Koma panali Aisiraeli ena amene anatsatila citsogozo ca Yehova. Mwacitsanzo, Yehova anati: “Kalebe . . . wakhala akunditsatila ndi mtima wonse.” (Ŵelengani Numeri 14:24.) Yehova anam’dalitsa Kalebe mwa kum’patsa malo amene iye anasankha m’dziko la Kanani. (Yos. 14:​12-14) Nawonso m’badwo wotsatila wa Aisiraeli unapeleka citsanzo cabwino pa nkhani yotsatila citsogozo ca Yehova. Yoswa ataloŵa m’malo mwa Mose monga mtsogoleli wa Aisiraeli, iwo “anayamba kumuopa monga mmene anaopela Mose masiku onse a moyo wake”. (Yos. 4:14) Zotulukapo zake, Yehova anawadalitsa mwa kuwaloŵetsa m’dziko limene anawalonjeza.—Yos. 21:​43, 44.

8. Fotokozani mmene Yehova anatsogolela anthu m’nthawi ya mafumu. (Onaninso cithunzi.)

8 Patapita zaka, Yehova anayamba kupatsa anthu ake oweluza kuti aziwatsogolela. Pambuyo pake, pomwe mafumu anayamba kulamulila, Yehova anasankha aneneli kuti azipeleka malangizo kwa anthu ake. Mafumu okhulupilika anali kutsatila upangili wocokela kwa aneneli. Mwacitsanzo, modzicepetsa Mfumu Davide analandila uphungu wocokela kwa mneneli Natani. (2 Sam. 12:​7, 13; 1 Mbiri 17:​3, 4) Mfumu Yehosafati anadalila citsogozo ca mneneli Yahazieli, ndipo analimbikitsa anthu a ku Yuda kuti ‘akhulupilile aneneli a Mulungu.’ (2 Mbiri 20:​14, 15, 20) Atapanikizika maganizo, Mfumu Hezekiya anafunsila upangili kwa mneneli Yesaya. (Yes. 37:​1-6) Nthawi iliyonse mafumuwa akatsatila citsogozo ca Yehova, anali kudalitsidwa, ndipo mtundu wonse unali kukhala wotetezeka. (2 Mbiri 20:​29, 30; 32:22). Zinali zoonekelatu kuti Yehova anali kuseŵenzetsa aneneli kutsogolela anthu ake. Ngakhale n’telo, mafumu oculuka, komanso anthu anakana aneneli a Yehova.—Yer. 35:​12-15.

Mfumu Hezekiya komanso mneneli Yesaya (Onani ndime 8)


MMENE YEHOVA ANATSOGOLELA AKHRISTU OYAMBILILA

9. Kodi Yehova anaseŵenzetsa ndani potsogolela Akhristu a m’zaka za zana loyamba? (Onaninso cithunzi.)

9 M’zaka za zana loyamba, Yehova anakhazikitsa mpingo wa Cikhristu. Kodi anali kuwatsogolela motani Akhristu oyambilila? Iye anaika Yesu kukhala mutu wa mpingo. (Aef. 5:23) Koma Yesu sanali kupeleka malangizo kwa mtumwi aliyense payekha-payekha. Anali kugwilitsa nchito atumwi, komanso akulu ku Yerusalemu kuti azitsogolela. (Mac. 15:​1, 2) Akulu ena anasankhidwa kuti azitsogolela m’mipingo.—1 Ates. 5:12; Tito 1:5.

Atumwi na akulu ku Yerusalemu (Onani ndime 9)


10. (a) Kodi Akhristu ambili a m’zaka za zana loyamba anali kuciona motani citsogozo ca Yehova? (Mac. 15:​30, 31) (b) N’cifukwa ciyani anthu ena m’nthawi za Baibo analephela kulemekeza anthu oimilako Yehova? (Onani danga lakuti “ Cifukwa Cake Anthu Ena Akana Umboni Woonekelatu.”)

10 Kodi Akhristu oyambilila anali kuciona motani citsogozoco? Ambili anali kutsatila mokondwela malangizo amene anali kupatsidwa. Mwacitsanzo, pa nthawi ina, iwo “anakondwela cifukwa ca mawu olimbikitsa” amene analandila. (Ŵelengani Machitidwe 15:​30, 31.) Nanga kodi Yehova wakhala akuwatsogolela motani anthu ake masiku ano?

MMENE YEHOVA AKUTITSOGOLELA MASIKU ANO

11. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Yehova wakhala akutsogolela anthu omuimilako masiku ano.

11 Yehova akupitilizabe kutsogolela anthu ake masiku ano. Wakhala akucita zimenezi kupitila m’Mawu ake, komanso Mwana wake, mutu wa mpingo. Kodi pali umboni woonetsa kuti Yehova akali kugwilitsa nchito anthu kumuimilako? Inde. Mwacitsanzo, ganizilani zomwe zinacitika pambuyo pa caka ca 1870. M’bale Charles Taze Russel na anzake anazindikila kuti caka ca 1914 cidzakhala caka cofunika kwambili pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu. (Dan. 4:​25, 26) Iwo anadalila ulosi wa m’Baibo kuti afike pa mfundo imeneyi. Kodi Yehova anali kuwatsogolela pomwe anali kufufuza m’Baibo? N’zosacita kufunsa. Mu 1914 zocitika za padziko zinatsimikizila kuti Ufumu wa Mulungu wayamba kulamulila. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse inabuka, ndipo kunalinso milili, zivomezi, komanso njala. (Luka 21:​10, 11) Yehova anali kuseŵenzetsadi amuna a Cikhristu amenewa kuthandiza anthu ake.

12-13. Kodi panacitika zotani pofuna kupititsa patsogolo nchito yolalikila pa nthawi ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse?

12 Ganizilaninso zomwe zinacitika pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. Pambuyo posanthula Chivumbulutso 17:​8, abale audindo kulikulu lathu anazindikila kuti nkhondoyo sidzatsogolela ku Aramagedo. M’malomwake, padzakhala nthawi yamtendele imene idzatsegula mipata yambili yolalikila. Ngakhale kuti zinali kuoneka zosathandiza pa nthawiyo, gulu la Yehova linakhazikitsa Sukulu ya Giliyadi kuti ithandize amishonale kuphunzitsa na kulalikila pa dziko lonse lapansi. Amishonale anali kutumizidwa ngakhale pa nthawi ya nkhondo. Kuwonjezela apo, kapolo wokhulupilika anapanga makonzedwe akuti pakhale Sukulu ya Utumiki b kuti iziphunzitsa onse m’mipingo kukhala alaliki, komanso aphunzitsi aluso. Makonzedwe amenewa anakonzekeletsa anthu a Mulungu nchito ya m’tsogolo.

13 Zocitika zimenezi zionetsa poyela kuti Yehova anali kutsogolela anthu ake pa nthawi yovuta imeneyi. Cicokeleni pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, anthu a Yehova m’maiko ambili anapezako mtendele komanso ufulu pogwila nchito yolalikila. Ndipo nchitoyi yapita patsogolo kwambili.

14. N’cifukwa ciyani tiyenela kutsatila malangizo ocokela ku gulu la Yehova, komanso kwa akulu osankhidwa? (Chivumbulutso 2:1) (Onaninso cithunzi.)

14 Masiku anonso, ziwalo za Bungwe Lolamulila zikupitiliza kuyang’ana kwa Khristu kaamba ka citsogozo. Amafuna kuti malangizo amene amapeleka kwa abale na alongo azikhala ogwilizana na cifunilo ca Mulungu. Ndipo amaseŵenzetsa oyang’anila madela, komanso akulu popeleka malangizo amenewa ku mipingo. c Akulu odzodzedwa ali “m’dzanja . . . lamanja” la Khristu. (Ŵelengani Chivumbulutso 2:1.) Akulu amenewa ni opanda ungwilo ndipo nthawi zina amalakwitsa. Mose, Yoswa, komanso atumwi anali kulakwitsa zinthu nthawi zina. (Num. 20:12; Yos. 9:​14, 15; Aroma 3:23). Ngakhale n’telo, Khristu akutsogolela kapolo wokhulupilika, komanso akulu osankhidwa, ndipo adzapitiliza kukhala nawo “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20). Cotelo, tili na zifukwa zomveka zokhalila na cidalilo m’citsogozo cimene Yesu akupeleka kupitila mwa awo amene anasankhidwa kuti azititsogolela.

Bungwe Lolamulila masiku ano (Onani ndime 14)


TIMAPINDULA TIKAMATSATILABE CITSOGOZO CA YEHOVA

15-16. Mwaphunzila ciyani ku zitsanzo za amene anatsatila citsogozo ca Yehova?

15 Tikamatsatilabe citsogozo ca Yehova, tidzalandila madalitso ngakhale masiku ano. Mwacitsanzo, m’bale Andy na mkazi wake Robyn anatsatila cilimbikitso cakuti akhale na umoyo wosalila zambili. (Mateyu 6:22.) Conco, anadzipeleka pa nchito zamamangidwe za gulu. Mlongo Robyn anati: “Takhalapo m’nyumba zing’ono-zing’ono zopanda khicini. Ngakhale kuti n’nali kukonda kujambula, n’nagulitsa zipangizo zanga zambili zomwe n’nali kuseŵenzetsa pojambula. N’nali kuzikonda ngako moti n’nalila pozigulitsa. Koma mofanana na Sara, mkazi wa Abulahamu, n’nali wotsimikiza mtima kuika maganizo anga pa zinthu za kutsogolo osati za kumbuyo.” (Aheb. 11:15) Kodi banjali linapindula motani? Mlongo Robyn anati: “Ndife okhutila podziŵa kuti tikupatsa Yehova zonse zimene tingathe. Tikamacita utumiki wathu, timakhala na mwayi wolaŵako mmene moyo udzakhalile m’dziko latsopano.” M’bale Andy anavomeleza kuti: “Ndife osangalala kuti tikuseŵenzetsa nthawi yathu, komanso mphamvu zathu popititsa patsogolo Ufumu wa Mulungu.”

16 Timapindulanso motani tikamatsatilabe citsogozo ca Yehova? Marcia atamaliza maphunzilo a ku sekondale anatsatila cilimbikitso cakuti ayambe upainiya wa nthawi zonse. (Mat. 6:33; Aroma 12:11) Iye anati: “N’napatsidwa sikolashipu ya zaka 4 ku yunivesite. Koma n’nali na zolinga zauzimu zimene n’nali kufuna kukwanilitsa mu utumiki wa Yehova. Conco n’nasankha kucita kakosi kuti niphunzile luso lina lake limene linganithandize pocita upainiya. N’cimodzi mwa zisankho zanzelu zimene n’napanga. Pali pano nikusangalala na upainiya wa nthawi zonse, komanso nchito yanga imanipatsa mpata wothandizako nchito za pa Beteli. Ndipo nikusangalanso na mautumiki ena apadela.

17. Ni madalitso ena ati amene tidzapeza tikapitilizabe kutsatila citsogozo ca Yehova? (Yesaya 48:​17, 18)

17 Nthawi zina timalandila uphungu wotiteteza ku mavuto omwe angabwele cifukwa cokondetsetsa zinthu zakuthupi, komanso ku zinthu zomwe zingatiphwanyitse malamulo a Mulungu. Timapenzanso madalitso tikatsatila citsogozo cimeneci. Timakhala na cikumbumtima coyela, ndipo timapewa mavuto ena. (1 Tim. 6:​9, 10) Tikatsatila citsogozoco, tidzatha kutumikila Yehova na mtima wonse, zimene zimabweletsa cimwemwe cacikulu, mtendele, komanso kukhala okhutila.—Ŵelengani Yesaya 48:​17, 18.

18. N’cifukwa ciyani muli wofunitsitsa kutsatila citsogozo ca Yehova?

18 Mosakailila, Yehova adzapitilizabe kugwilitsa nchito anthu omuimilako popeleka citsogozo pa cisautso cacikulu, komanso mu ulamulilo wa zaka 1,000. (Sal. 45:16) Kodi tidzapitilizabe kutsatila citsogozo ngakhale pamene sitinagwilizane nazo? Zidzadalila kwambili pa mmene timacitila panopa tikalandila citsogozo ca Yehova. (Yes. 32:​1, 2; Aheb. 13:17) Conco, tiyeni nthawi zonse tipitilize kutsatila citsogozo ca Yehova kuphatikizapo copelekedwa na amuna amene anasankhidwa kuti azitiyang’anila. Timatelo podziŵa kuti tili na zifukwa zomveka zodalila Wotilondolela Njila wathu, Yehova, amene amatipewetsa ngozi zauzimu na kutitsogolela kumene tikupita—ku moyo wosatha m’dziko latsopano.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yehova anawatsogolela motani Aisiraeli?

  • Kodi Yehova anawatsogolela motani Akhristu oyambilila?

  • Timapindula motani tikatsatila citsogozo ca Yehova masiku ano?

NYIMBO 48 Kuyenda ndi Yehova Tsiku na Tsiku

a Yehova anasankhanso mngelo “amene anali kuyenda patsogolo pa Aisiraeli” kukawafikitsa m’Dziko Lolonjezedwa. Mwacionekele, mngelo ameneyo anali Mikayeli—Yesu asanabadwe monga munthu pa dziko lapansi—Eks. 14:19; 32:34.

b Pambuyo pake inadzachedwa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Masiku ano inaphatikiziwa kukhala mbali ya msonkhano wa mkati mwa mlungu.

c Onani bokosi lakuti “Udindo wa Bungwe Lolamulila” mu Nsanja ya Mlonda ya February 2021, tsamba 18.