NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA February 2024

Maganizo ino ili na nkhani zophunzila kuyambila pa April 8–May 5, 2024.

NKHANI YOPHUNZILA 5

“Sindidzakusiyani Kapena Kukutayani Ngakhale Pang’ono”!

Yophunzila mu mlungu wa April 8-14, 2024.

NKHANI YOPHUNZILA 6

“Tamandani Dzina la Yehova”

Yophunzila mu mlungu wa April 15-21, 2024.

NKHANI YOPHUNZILA 7

Zimene Tikuphunzilapo kwa Anazili

Yophunzila mu mlungu wa April 22-28, 2024.

NKHANI YOPHUNZILA 8

Musaleke Kutsatila Citsogozo ca Yehova

Yophunzila mu mlungu wa April 29–​May 5, 2024.

Pezani Cimwemwe Poyembekezela Yehova Moleza Mtima

Anthu ambili amalefulidwa na dongosolo lino la zinthu pomwe akuyembekezela kuti Yehova acitepo kanthu pa nthawi yake. N’ciyani cingatipeputsileko zinthu pamene tikuyembekezela, na kutithandiza kupeza cimwemwe pamene ticita zimenezi?

Ziwalo Ziŵili Zatsopano za Bungwe Lolamulila

Pa Citatu, January 18, 2023, panapelekewa cilengezo cakuti M’bale Gage Fleegle na M’bale Jeffrey Winder aikidwa kuti azitumikila monga ziwalo za Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova.

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Baibo imatiululila ciyani za mphamvu za Yehova zokwanitsa kunenelatu zamtsogolo?

Kodi Mudziŵa?

Ganizilani zifukwa zitatu zimene ziyenela kuti zinapangitsa olemba Baibo kucita zimenezi.

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU

Pezani Cuma Cauzimu Comwe Mungaseŵenzetse