Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu Amamvela Bwanji Akaona Kuti Muvutika?

Kodi Mulungu Amamvela Bwanji Akaona Kuti Muvutika?

Anthu ena amakhulupilila kuti Mulungu saona mavuto awo ndipo sizimukhudza.

ONANI ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

  • Mulungu amaona komanso amasamala za ise

    “Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwaculuka padziko lapansi . . . , ndipo zinam’pweteka kwambili mumtima.”—Genesis 6:5, 6.

  • Mulungu adzacotsapo mavuto onse

    “Patsala kanthawi kocepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:10, 11.

  • Zimene Mulungu amakufunilani

    “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizila zokupatsani mtendele osati masoka, kuti mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watelo Yehova. ‘Mudzaitanila pa ine komanso mudzabwela ndi kupemphela kwa ine ndipo ine ndidzakumvetselani.’”—Yeremiya 29:11, 12.

    “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.