Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ndinu ofunika kwambili.”—MATEYU 10:31

Kodi Mulungu Amakudelani Nkhawa?

Kodi Mulungu Amakudelani Nkhawa?

ZIMENE CILENGEDWE CIMATIPHUNZITSA

Mwana akangobadwa, ola loyamba limakhala nthawi yofunika kwambili kwa iye. Cifukwa ciani? Panthawiyi, mayi amafunika kukhudzana na mwana wake wakhandayo mwa kumuonetsa cikondi cake. Kukhudzana mwacikondi kumeneku, kumathandiza kuti mwana wakhandayo ayambe kukula bwino. *

N’ciani cimapangitsa mayi kusamalila khanda lake mwacikondi likangobadwa? Malinga n’zimene pulofesa wina dzina lake Jeannette Crenshaw anafotokoza m’buku yakuti, The Journal of Perinatal Education, mwana akangobadwa, mahomoni ochedwa oxytocin amaculuka m’thupi la mayi na “kum’pangitsa kuonetsa cikondi kwambili kwa khanda lake pamene amugwila, kumuyang’ana, komanso pomuyamwitsa.” Mahomoni ena “amathandiza mayi kukhudzika mtima na khanda lake,” komanso kuceza naye kwambili. N’cifukwa ciani izi n’zocititsa cidwi?

Mgwilizano umene umakhalapo pakati pa mayi na khanda lake unakonzedwa na Mlengi wathu wacikondi, Yehova Mulungu. * Mfumu Davide anayamikila Mulungu cifukwa ‘comutulutsa m’mimba,’ komanso kumucititsa kudzimva wotetezeka pamene amayi ake anali kumufungatila mwacikondi. Anapemphela kuti: “Ndinaponyedwa m’manja mwanu kucokela m’mimba. Kuyambila ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.”—Salimo 22:9, 10.

GANIZILANI IZI: Ngati Mulungu analenga thupi la mayi modabwitsa kwambili conco, kuti azisamalila khanda lake mwacikondi, komanso kum’patsa zofunikila, kodi si zomveka kuti Mulungu amatisamalila aliyense payekha, monga ‘mbadwa zake’?—Machitidwe 17:29.

ZIMENE BAIBO IMATIPHUNZITSA PONENA ZA CISAMALILO CA MULUNGU

Yesu Khristu, amene amam’dziŵa bwino kwambili Mlengi kupambana wina aliyense, anati: “Kodi mpheta ziwili si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kocepa mphamvu? Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwelenga. Conco musacite mantha: Ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zoculuka.”—Mateyu 10:29-31.

Ambili a ife sitiikako nzelu tikaona kambalame kakang’ono kakudutsa. Sitiikilako nzelu ngakhale kamodzi kagwe pansi. Koma Atate wathu wakumwamba amakadziŵa kalikonse pakokha-pakokha! Ngakhale mbalame zitaculuka bwanji, sizingakhale zofunika kwambili kuposa munthu. Conco, phunzilo apa ni yoonekelatu: “Musacite mantha” kuti Mulungu samakudelani nkhawa. M’malomwake, iye amadela nkhawa kwambili za imwe!

Mulungu amatidela nkhawa komanso kutiyang’anila mwacikondi

Malemba amatitsimikizila kuti

  • “Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.” —MIYAMBO 15:3.

  • “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—SALIMO 34:15.

  • “Ndidzakondwela ndi kusangalala cifukwa ca kukoma mtima kwanu kosatha, pakuti mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwela.”—SALIMO 31:7.

“N’NALI KUONA MONGA YEHOVA SANIKONDA”

Kodi zingakhale zothandiza tikadziŵa kuti Mulungu amatidela nkhawa komanso kutiyang’anila mwacikondi? Inde. Malinga n’zimene Hannah, * wa ku England anakamba zingakhale zothandiza kwambili. Iye anati:

“Nthawi zambili, n’nali kuona monga Yehova sanikonda, komanso kuti mapemphelo anga sayankhidwa. Zinali conco cifukwa n’nalibe cikhulupililo. N’nali kuonanso monga akunilanga, komanso kuninyalanyaza cifukwa ndine wosafunika. N’nali kuganizanso kuti Mulungu sanisamalila.”

Koma manje, Hannah sakaikilanso kuti Yehova amam’dela nkhawa, komanso kum’konda. N’ciani cinam’thandiza kusintha? Iye anati: “N’nayamba kusintha pang’ono pang’ono. Nikumbukila nkhani ina ya Baibo imene n’namvetsela zaka zambili zapita. Inali kukamba za dipo la Yesu. Nkhaniyo inanikhudza kwambili. Inanitsimikizila kuti Yehova amanikonda. Nikaonanso kuti mapemphelo anga akuyankhidwa, nthawi zambili nimacita kugwetsa misozi poona kuti Yehova amanikonda. Kuŵelenga Baibo na kupezeka ku misonkhano yacikhristu, kwaniphunzitsanso zambili za Yehova, makhalidwe ake, na kuti amatidela nkhawa. Pali pano, ndine wotsimikiza kuti Yehova amatidela nkhawa, na kuti amatikonda tonse. Komanso ni wofunitsitsa kutisamalila aliyense payekha-payekha.”

Zimene Hannah anakamba n’zolimbikitsa. Koma n’ciani cingakuthandizeni kutsimikiza kuti Mulungu amakumvetsetsani, na kuti amadziŵa mmene m’mamvelela? Nkhani yotsatila idzayankha funso imeneyi.

^ Azimayi amene amavutika maganizo akabeleka, cimawavuta kuti aonetse cikondi kwa khanda lawo. Koma sayenela kudziimba mlandu kuti iwo ndiwo ali na vuto. Malinga na zimene inakamba Bungwe la U.S. National Institute of Mental Health, kuvutika maganizo “kumabwela cifukwa ca zocitika zina zakuthupi komanso zokhudza maganizo, . . . koma sikuti pali zimene mayi amacita kapena kulephela kucita.” Kuti mudziŵe zambili pa nkhani imeneyi ŵelengani nkhani yakuti, “Ndinagonjetsa Vuto Langa Losokonezeka Maganizo Nditabereka” mu Galamukani! ya Chichewa ya August 8, 2002.

^ Yehova ni dzina la Mulungu lopezeka m’Baibo.—Salimo 83:18.

^ Maina ena m’nkhani zimenezi asinthidwa.