Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI TINGAPEZE KUTI CITONTHOZO?

Tonse Timafunika Citonthozo

Tonse Timafunika Citonthozo

Kodi pamene munali mwana munagwapo? Mwina pamene munagwa munadziphweteka dzanja kapena mwendo. Kodi mukumbukila mmene amayi anu anakutonthozelani? N’kutheka kuti anatsuka cilondaco n’kumangapo. Munalila, koma amayi anu atakutonthozani ndi kukukupatilani mwacikondi, munamvelako bwino. N’zoonekelatu kuti wokutonthozani sanali kusoŵa panthawiyo.

Koma pamene tikula zinthu zimayamba kuvuta paumoyo. Mavuto amaculuka, koma citonthozo cimasoŵa. N’zomvetsa cisoni kuti mavuto amene anthu akulu-akulu amakumana nawo, nthawi zambili amavuta kuthetsa. Onani zitsanzo izi.

  • Kodi munakhumudwapo cifukwa ca kucotsedwa nchito? Julian anakamba kuti atacotsedwa nchito anali na nkhawa yaikulu. Anali kudzifunsa kuti, ‘Nisamalila bwanji banja langa? N’cifukwa ciani kampani yaona kuti ndine wosafunika pambuyo poseŵenza mwamphamvu kwa zaka zambili?’

  • Mwina ndinu wokhumudwa cifukwa ca kutha kwa cikwati canu. Raquel anafotokoza kuti: “Pamene mwamuna wanga ananisiya mwadzidzidzi miyezi 18 yapitayo, n’nali na cisoni kwambili. N’namvela monga mtima wanga wang’ambika. Cinaniŵaŵa kwambili, ndipo n’nakhumudwa.”

  • Mwina muli na matenda aakulu ndipo muona kuti palibe cizindikilo cakuti mucila. Nthawi zina mungamvele monga mmene Yobu wakale anamvelela. Iye anati: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Yobu 7:16) Mwinanso mumamvela mofanana ndi mmene Luis, mwamuna wa zaka za m’ma 80, amamvelela. Iye anakamba kuti: “Nthawi zina nimaganiza kuti cimene catsala ni kufa cabe.”

  • Mwina mufuna citonthozo cifukwa munthu wina amene munali kukonda anamwalila. Robert anafotokoza kuti: “Mwana wanga atamwalila pa ngozi ya ndeke, poyamba sin’nakhulupilile. Pambuyo pake, n’namva ululu ngati umene Baibulo imauyelekezela na ‘lupanga lalitali lolasa moyo wako.’—Luka 2:35

Robert, Luis, Raquel, ndi Julian anapeza citonthozo, ngakhale kuti anakumana ndi mavuto aakulu. Anapeza citonthozo ceni-ceni kwa Mulungu Wamphamvuyonse. Kodi Mulungu amatonthoza bwanji? Kodi nanunso angakutonthozeni?