NSANJA YA MLONDA Na. 5 2016 | Kodi Tingapeze Kuti Citonthozo?

Tonse timafunika kutonthozedwa na Mulungu, maka-maka pa nthawi ya mavuto. Magazini iyi ikamba mmene Mulungu amatonthozela anthu amene akumana na mavuto.

NKHANI YA PACIKUTO

Tonse Timafunika Citonthozo

Mungapeze kuti citonthozo ngati muli na cisoni kaamba ka imfa ya munthu amene mumakonda, kapena ngati muli na vuto la matenda, cikwati, kapena nchito?

NKHANI YA PACIKUTO

Mmene Mulungu Amatitonthozela

Zinthu zinayi zimene zingathandize anthu amene akukumana na mavuto.

NKHANI YA PACIKUTO

Kupeza Citonthozo pa Nthawi Yovuta

Mmene anthu ena anapezela thandizo pa nthawi yovuta kwambili.

TENGELANI CIKHULUPILILO CAWO

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

N’ciani cinathandiza Davide kugonjetsa Goliyati? Tingaphunzile ciani pa nkhani ya Davide?

Kodi N’zoona Kuti Davide Anamenyana ndi Goliyati?

Anthu ena otsutsa amakamba kuti nkhani imeneyi ni yabodza. Kodi ali na umboni wokwanila pa nkhani imeneyi?

BAIBO IMASINTHA ANTHU

N’nali Woipa Mtima Kwambili ndi Waciwawa

N’ciani cinacititsa munthu wokonda ndewo wa ku Mexico kusintha umoyo wake?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Mungadabwe mukadziŵa yankho lake.