Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MAVUTO AMENE ALIPO

Zimene Zapangitsa Anthu Kusakhala Mwamtendele ndi Motetezeka

Zimene Zapangitsa Anthu Kusakhala Mwamtendele ndi Motetezeka

“Anthu masiku ano apita patsogolo kwambili m’zipangizo za makono, nkhani za sayansi komanso zacuma. . . Ngakhale n’conco, n’zodabwitsa kuti nkhani zandale na zacuma zaipilatu. Komanso kuwononga zacilengedwe kwafika pacimake.”—The Global Risks Report 2018, World Economic Forum

N’CIFUKWA CIANI AKATSWILI ALI NA NKHAWA ZOKHUDZA TSOGOLO LATHU, KOMANSO DZIKO LAPANSI? TIYENI TIONE ENA MWA MAVUTO AMENE TIKUKUMANA NAWO.

  • UPANDU WA PA INTANETI: Nyuzipepa ina ya ku Australia inati: “Kuposa na kale lonse, intaneti yakhala malo oopsa kuyendapo. Akhala malo opezekapo kwambili anthu ogona ana, ovutitsa anzawo, mbava za pa intaneti, komanso oyambitsilapo mikangano. Kuba zinthu zodziŵikitsa munthu nakonso kukuwonjezeleka kwambili pa dzikoli. . . Intaneti yapeleka mpata kwa anthu kuti azicita zinthu zoipa kwambili, kuŵapangitsa kukhala ankhanza kosaneneka.”

  • KUSIYANA PA ZACUMA: Malinga na lipoti la bungwe la Oxfam International, anthu olemela kwambili pa dziko lapansi ali 8 cabe, cakuti cuma cawo n’colingana ndi ca anthu okwanila 3.6 biliyoni osauka pa dziko. Inakambanso kuti: “Kusayenda bwino kwa zacuma, kwapangitsa kuti olemela alemeleletu, osauka asaukiletu. Ndipo amene amavutika kwambili ni azimayi.” Ena amacita mantha kuti kusiyana kumeneku kungabutse zipolowe.

  • NKHONDO NA KUCITILANA ZANKHANZA: Anthu oposa 68 miliyoni amathaŵa kusiya nyumba zawo, cifukwa ca nkhondo na kucitilidwa zankhanza. Lipoti la mu 2018 la bungwe la United Nation Refugee Agency linati: “Anthu othaŵa kwawo awonjezeka kwambili kuposa kale lonse. Ndipo zioneka kuti pa masekondi aŵili alionse, munthu mmodzi amathaŵa kwawo.”

  • KUWONONGA ZACILENGEDWE: Lipoti la mu 2018 linati: “Nyama na zomela za mitundu yosiyana-siyana, zikuwonongedwa pamlingo waukulu kwambili. Kuwonongedwa kwa mphepo, komanso madzi a m’nyanja nakonso kukupeleka ciopsezo cacikulu ku thanzi la anthu.” Kuwonjezela apo, pali tudoyo tumene tumathandiza zomela kubala zipatso. M’maiko ena tudoyo tumenetu twayamba kucepa kwambili. Mwa ici, asayansi lomba akucenjeza kuti cilengedwe cingawonongeke kothelatu.

Kodi n’zotheka kusintha zinthu kuti dzikoli likhale lamtendele komanso lotetezeka? Ena amaona kuti cothandiza ni kulandila maphunzilo. Ngati n’conco, kodi maphunzilo amenewo angakhale otani? Nkhani zotsatila zidzayankha mafunso amenewa.