Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BOMA LIMENE LIDZABWELETSA MTENDELE WENI-WENI

‘Ndipo Mtendelewo Sudzatha’

‘Ndipo Mtendelewo Sudzatha’

Bungwe la United Nations likulimbikitsa “anthu onse kukhala ogwilizana,” olemekeza maufulu a anthu, komanso osamalila zacilengedwe. Cifukwa ciani? M’magazini yochedwa UN Chronicle ya bungweli, Maher Nasser anati, “Kusintha kwa nyengo, magulu aupandu, kuonjezeka kwa kupondelezana, nkhondo zosatha, kuculuka kwa anthu othaŵa kwawo, ucigaŵenga, matenda oyambukila na zina zaconco, zimakhudza. . . anthu m’dziko lililonse.”

Anthu ena afika polimbikitsa mfundo yakuti pakhale boma la pa dziko lonse. Ena mwa iwo ni Dante wa ku Italy, amene anali katswili wa zamaphunzilo, mlembi wa ndakatulo, komanso wochuka m’zandale. Wina anali Albert Einstein amene anali katswili wasayansi. Dante anali kukhulupilila kuti mtendele sungakhalitse m’dziko logaŵikana pa zandale. Pogwila mawu a Yesu Khristu, iye anati: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha.”—Luka 11:17.

Mabomba aŵili a nyukiliya anaphulitsidwa pa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Nkhondoyo itatha, Albert Einstein analembela kalata nthambi ya bungwe la United Nations yochedwa General Assembly. Kalatayo inafalitsidwa kuti onse aiŵelenge. Ndipo inati, “Bungwe la United Nations lifunika kucitapo kanthu mwamsanga, pokhazikitsa mfundo zobweletsa citetezo kwa anthu onse, ndi kukhazikitsa boma lodalilika la pa dziko lonse.”

Koma kodi andale amene angapange boma lamphamvu limenelo, tingaŵadalile kuti sangacite zaciphuphu, kulephela kucita zinthu zina, na kupondeleza ena? Kapena naonso angakhale oipa monga olamulila ena? Mafunso amenewa atikumbutsa mawu a Lord Acton, katswili wolemba mbili yakale wa ku England. Iye anati: “Mphamvu za ulamulilo zingapangitse munthu kukhala woipa, ndipo zikaculuka kwambili angaipenso kwambili.”

Kuti tikhale pa mtendele weni-weni tifunika kukhala ogwilizana. Koma kodi colinga cimeneci cingakwanilitsidwe motani? Kodi cingakwanilitsikedi? Baibo imayankha kuti inde cingakwanilitsike, ndipo cidzakwanilitsikadi. Motani? Osati na boma la pa dziko lonse lopangidwa ndi anthu andale amene ni acinyengo. Koma zidzatheka na boma lopangidwa na Mulungu. Kuwonjezela apo, mu ufumu umenewo Mulungu adzaseŵenzetsa mphamvu zake kulamulila cilengedwe cake. Kodi ni boma iti imeneyo? Baibo imachula dzina la boma limenelo kuti “Ufumu wa Mulungu.”—Luka 4:43.”

“UFUMU WANU UBWELE”

M’pemphelo lake lacitsanzo, Yesu Khristu anali kuganiza za Ufumu wa Mulungu pamene anati: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike . . . pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Inde, Ufumu wa Mulungu udzaonetsetsa kuti cifunilo ca Mulungu cacitika pa dziko lapansi. Osati cifunilo ca anthu ongofuna ulamulilo cabe, komanso odzikonda.

Ufumu wa Mulungu umachedwanso kuti “Ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 5:3.) Cifukwa? Ngakhale kuti udzalamulila pa dziko lapansi, sudzalamulila kucokela pa dziko lapansi. Koma udzalamulila kucokela kumwamba. Ganizilani cabe mmene zinthu zidzakhalila. Boma la pa dziko lonse limeneli silidzafunikila thandizo la ndalama. Izi zidzakhala zotsitsimula kwambili kwa nzika za pa dziko lapansi za ufumuwo!

Ufumu wa Mulungu ni ulamulilo wacifumu. Yesu Khristu ndiye Mfumu yake, ndipo anapatsidwa ulamulilo na Mulungu. Pokamba za Yesu, Baibo imati:

  • “Paphewa pake padzakhala ulamulilo [boma] . . . Ulamulilo wake . . . udzafika kutali ndipo mtendele sudzatha.”—Yesaya 9:6, 7.

  • “Kenako anamupatsa ulamulilo, ulemelelo, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenelo zosiyanasiyana azimutumikila. Ulamulilo wake . . . sudzatha.”—Danieli 7:14.

  • “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye [Mulungu] wathu ndi wa Khristu wake.”—Chivumbulutso 11:15.

Poyankha pemphelo lacitsanzo la Yesu, Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa mokwanila cifunilo ca Mulungu pa dziko lapansi. Mu ulamulilo umenewo, anthu onse adzaphunzila kusamalila dziko kuti likhale labwino, na kuti pakhale zamoyo zambili.

Koposa zonse, Ufumu wa Mulungu udzapeleka maphunzilo kwa nzika zake. Onse adzaphunzitsidwa mfundo zofanana. Sipadzakhala kusagwilizana kapena kugaŵikana. Yesaya 11:9 imati: “Sizidzavulazana kapena kuwonongana . . . cifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazila nyanja.”

Anthu pa dziko lonse adzakhala ogwilizana, komanso adzakhala pa mtendele wina na mnzake. Izi n’zimene bungwe la United Nations lalephela kukwanilitsa. Salimo 37:11 imati: “Adzasangalala ndi mtendele woculuka.” M’kupita kwa nthawi, mawu monga “upandu,” “kuwononga cilengedwe,” “umphawi,” komanso “nkhondo,” sadzamvekanso pakamwa pathu. Koma kodi zimenezi zidzacitika liti? Kodi Ufumu wa Mulungu udzayamba liti kulamulila pa dziko lapansi? Kodi Ufumu wa Mulungu udzalamulila motani? Nanga kodi mungapindule bwanji na ulamulilo wake? Tiyeni tione.