Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 52

Asilikali a Yehova Amoto

Asilikali a Yehova Amoto

Beni-hadadi Mfumu ya Siriya, anali kuukila Isiraeli kaŵili-kaŵili. Koma mneneli Elisa anali kucenjeza mfumu ya Isiraeli nthawi zonse kuti ithaŵe. Conco Beni-hadadi anaganiza zogwila Elisa. Atafufuza anadziŵa kuti Elisa anali mu mzinda wa Dotana. Ndiye anatuma asilikali ake kuti akam’gwile.

Asilikali acisiriya aja anafika ku Dotana usiku. M’mawa mwake, mtumiki wa Elisa atacoka panja, anangoona kuti mzindawo wazingidwa na asilikali ambili-mbili. Anacita mantha na kufuula kuti: ‘A Elisa, tidzacita bwanji?’ Elisa anamuuza kuti: ‘Ife tili na ambili kumbali yathu kuposa amene ali kumbali yawo.’ Pamenepo, Yehova anatsegula maso a mtumiki wa Elisa, ndipo anaona kuti mapili ozungulila mzindawo, anali odzala na mahosi na magaleta ankhondo oyaka moto.

Pamene asilikali acisiriya anayesa kugwila Elisa, iye anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize. Mwadzidzidzi, ngakhale kuti asilikaliwo anali kuona, anasokonezeka cakuti sanadziŵenso kumene anali. Ndiyeno Elisa anaŵauza kuti: ‘Mwataika, mwabwela ku mzinda wolakwika. Tiyeni nikupelekeni kwa munthu amene mufuna.’ Conco iwo anatsatila Elisa mpaka ku Samariya kwa mfumu ya Isiraeli.

Apa lomba asilikali acisiriya anazindikila kumene anali, koma mocedwa, anali kale m’manja mwa mfumu ya Isiraeli. Ndiye mfumuyo inafunsa Elisa kuti: ‘Kodi niŵaphe?’ Kodi Elisa anapezelapo mwayi wokhaulitsa asilikaliwo, amene anafuna kumucita zoipa? Iyai. Elisa anati: ‘Iyai musaŵaphe. Apatseni cakudya, akadya muŵalole apite kwawo.’ Conco, mfumuyo inawakonzela phwando lalikulu. Pambuyo pake inaŵalola kupita kwawo.

“Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.”—1 Yohane 5:14