Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 20

Milili 6 Yokonkhapo

Milili 6 Yokonkhapo

Mose na Aroni anapita kukauza Farao uthenga wa Mulungu kuti: ‘Ngati sudzalola anthu anga kupita, nidzatumiza tudoyo toyamwa magazi m’dziko lako.’ M’nyumba zonse za Aiguputo, za olemela komanso osauka, munadzala tudoyo utu. Tunali paliponse m’dziko lonse. Koma kudela la Goseni, kumene Aisiraeli anali kukhala, kunalibe tudoyo utu. Kuyambila pa mlili uwu wa namba 4, yonse yokonkhapo inali kugwela Aiguputo cabe. Ndiyeno Farao anapapata kuti: ‘Condelela Yehova kuti acotse tudoyo utu, ndipo nidzalola kuti anthu anu apite.’ Koma pamene Yehova anacotsa tudoyoto, Farao anacinjanso maganizo. Kodi Farao anali wokanga?

Yehova anati: ‘Ngati Farao sadzalola anthu anga kupita, nyama za Aiguputo zonse zidzadwala na kufa.’ M’maŵa mwake, nyama zinayamba kufa. Koma nyama za Aisiraeli sizinafe. Farao anacitabe mwano, ndipo sanawalole kupita.

Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti apitenso kwa Farao kukamwaza phulusa m’mwamba. Phulusalo linasanduka fumbi, cakuti mphepo yonse inali fumbi lokha-lokha kwa Aiguputo onse. Aiguputo onse na nyama zawo anakhala na zilonda zoŵaŵa cifukwa ca fumbi limenelo. Koma Farao anakanilatu kuti Aisiraeli apite.

Yehova anatumanso Mose kwa Farao kukamuuza kuti: ‘Kodi ukali kuletsa kuti anthu anga apite? Mailo kudzagwa cimvula ca matalala.’ Ndipo tsiku lotsatila, Yehova anabweletsa cimvula ca matalala, mabingu, na moto. Cinali cimvula cimene Aiguputo sanacionepo. Cinawononga mitengo na mbewu zonse, koma osati m’dela la Goseni. Farao anati: ‘Pemphani Yehova kuti aletse cimvula ici, kuti mucoke!’ Koma mvula na matalala zitangoleka, Farao anasinthanso maganizo ake.

Lomba Mose anati: ‘Tsopano dzombe lidzadya zomela zilizonse zimene cimvula ca matalala cinasiyako.’ Cigulu ca dzombe cinadya ciliconse cimene cinatsala m’minda na m’mitengo. Farao anacondelela kuti: ‘Pemphani Yehova kuti acotse vidzombe ivi.’ Koma Yehova atacotsa dzombelo, Farao anacitabe mwano.

Yehova anauza Mose kuti: ‘Tambasula dzanja lako ulate kumwamba.’ Pamenepo kumwamba kunacita cimdima candiweyani. Kwa masiku atatu, Aiguputo sanali kuona ciliconse kapena kuonana. Koma kunyumba za Aisiraeli kunalibe mdima.

Farao anati kwa Mose: ‘Iwe ndi anthu ako cokani, pitani. Koma musatenge nyama zanu.’ Koma Mose anati: ‘Titenga nyama zathu kuti tikapelekele nsembe kwa Mulungu wathu.’ Farao anakwiya kwambili. Anafuula kuti: ‘Coka pano! Nikadzakuonanso, nidzakupha.’

“Anthu inu mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikila Mulungu ndi amene sanatumikilepo Mulungu.”—Malaki 3:18