Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 17

Kodi Oyang’anila Dela Amatithandiza m’Njila Ziti?

Kodi Oyang’anila Dela Amatithandiza m’Njila Ziti?

Ku Malawi

Kagulu ka ulaliki

Alalikila

Miting’i ya akulu

Malemba Acigiriki Acikristu amatiuza za Baranaba ndi mtumwi Paulo. Amuna amenewa anatumikila monga oyang’anila oyendela, ndipo anali kucezela mipingo. Kodi n’ciani cimene cinawasonkhezela kucita zimenezi? Anali kudela nkhawa umoyo wa ku uzimu wa abale ao. Paulo anakamba kuti iye anafuna ‘kubwelela kuti akacezele abale’ ndi kuona kuti ali bwanji. Iye anali wokonzeka kuyenda makilomita ambili kuti akawalimbikitse. (Machitidwe 15:36) Cimeneci ndiye colinga ca oyang’anila oyendela masiku ano.

Amabwela kudzatilimbikitsa. Woyang’anila dela aliyense amayendela mipingo pafupi-fupi 20, ndipo amathela wiki imodzi pampingo uliwonse, kaŵili pa caka. Timalimbikitsidwa kwambili ndi abale amenewa ndi akazi ao, ngati ni okwatila. Oyang’anila dela ndi akazi ao amayesetsa kudziŵana ndi onse, acicepele ndi acikulile omwe. Iwo amafuna kulalikila ndi ife ndi kupita nafe ku maphunzilo a Baibo. Oyang’anila amenewa amacita maulendo aubusa pamodzi ndi akulu, ndipo kuti atilimbikitse, amakamba nkhani pamisonkhano ya mpingo ndi pamisonkhano ikulu-ikulu.—Machitidwe 15:35.

Amakhala ndi cidwi pa aliyense. Oyang’anila dela amafuna kudziŵa umoyo wa ku uzimu wa mipingo yonse. Amakumana ndi akulu ndi atumiki othandiza kuti aone mmene mpingo wapitila patsogolo ndi kuwathandiza mmene angagwilile bwino nchito zao. Amathandiza apainiya kupeza cipambano pa utumiki wao, ndipo amakonda kudziŵana ndi atsopano ndi kumva mmene akupitila patsogolo m’coonadi. Aliyense wa abale amenewa amadzipeleka monga wanchito mnzathu kuti ‘atithandize.’ (2 Akorinto 8:23) Tizitsanzila cikhulupililo cao ndi kudzipeleka kwao kwa Mulungu.—Aheberi 13:7.

  • N’cifukwa ciani oyang’anila dela amacezela mipingo?

  • Kodi amatithandiza pambali ziti akamacezela mpingo?