Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 19

Kodi Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu Ndani?

Kodi Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu Ndani?

Tonse timapindula ndi cakudya ca ku uzimu

Imfa ya Yesu itayandikila, iye anakambitsilana mwamseli ndi ophunzila ake anayi. Maina ao ni Petulo, Yakobo, Yohane, ndi Andireya. Pamene Yesu anali kufotokoza cizindikilo ca kukhalapo kwake m’masiku otsiliza, anafunsa funso lofunika kwambili lakuti: “Ndani kweni-kweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa cakudya pa nthawi yoyenela?” (Mateyu 24:3, 45; Maliko 13:3, 4) Yesu anali kutsimikizila ophunzila ake kuti iye monga “mbuye” wao, adzasankha anthu amene azigaŵila otsatila ake cakudya ca ku uzimu m’nthawi ya mapeto. Kodi kapolo ameneyu ndani?

Ni kagulu kocepa ka otsatila a Yesu. “Kapolo” ameneyu ni Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. Amapeleka cakudya ca pa nthawi yake kwa alambili a Yehova. Timadalila kapolo wokhulupilika kuti azitipatsa “cakudya cokwanila pa nthawi yake.”—Luka 12:42.

Amayang’anila nyumba ya Mulungu. (1 Timoteyo 3:15) Yesu anapatsa kapolo udindo waukulu woyang’anila nchito ya mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova, monga kusamalila cuma cake, kutsogolela nchito yolalikila, ndi kutiphunzitsa kupitila m’mipingo yathu. Conco, kuti “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” atipatse zofunikila pa nthawi yake, amagaŵila cakudya ca ku uzimu kupitila m’zofalitsa zimene timagwilitsila nchito mu ulaliki, ndiponso kupitila m’misonkhano yathu ya mpingo ndi misonkhano yaikulu.

Kapolo ameneyu ni wokhulupilika pa nkhani yotsatila coonadi ca m’Baibo ndi pa nchito imene anapatsidwa yolalikila uthenga wabwino, ndipo ni wanzelu cifukwa amadziŵa kusamalila zinthu za Yesu padziko lapansi. (Machitidwe 10:42) Yehova akudalitsa nchito ya kapolo ndi cionjezeko cacikulu ndi cakudya ca ku uzimu ca mwana alilenji.—Yesaya 60:22; 65:13.

  • Kodi Yesu anasankha ndani kuti azigaŵila ophunzila ake cakudya ca ku uzimu?

  • Kodi kapolo ni wokhulupilika ndipo ni wanzelu m’njila ziti?