Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Paladaiso Ili Pafupi!

Paladaiso Ili Pafupi!

Phunzilo 6

Paladaiso Ili Pafupi!

Voipa vamene vicitika padziko lapansi vionetsa kuti Paladaiso ili pafupi. Baibo inakambilatu kuti pamene Paladaiso ili pafupi kubwela, padzakhala nthawi yovuta kwambili. Nthawi imeneyo ndiye ino! Onani vinthu vina vamene Baibo inakambilatu kuti vidzacitika:

Nkhondo Zikuluzikulu. “Mtundu umodzi wa anthu udzaukilana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Ulosi umenewu wakwanilitsika. Kuyambila mu caka ca 1914, kwacitika nkhondo ziŵili za padziko lonse na nkhondo zina zing’ono-zing’ono zambili. Ndipo anthu mamiliyoni ambili afa m’nkhondo zimenezi.

Kuwanda kwa matenda. Padzakhala “milili [matenda owanda] m’malo akuti akuti.’’ (Luka 21:11) Kodi zimenezi zacitika? Inde. Matenda a kansa, matenda a mtima, cifuwa ca TB, maleliya, AIDS, na matenda ena amapha anthu mamiliyoni ambili.

Njala. Padziko lonse lapansi pali anthu ambili amene alibe cakudya cokwanila. Caka ciliconse anthu mamiliyoni amafa na njala. Cimeneci ni cina codziŵila kuti Paladaiso ili pafupi. Baibo imakamba kuti: “Padzakhala njala.”—Marko 13:8.

Zivomezi. ‘Kudzakhala . . . zivomezi m’malo akuti akuti.’ (Mateyu 24:7) Nazo izi zacitika m’nthawi yathu. Kuyambila mu 1914, zivomezi zapha anthu opitilila miliyoni imodzi.

Anthu oipa. Anthu adzakhala “okonda ndalama” ndi “odzikonda okha.” Adzakhala “okonda zokondweletsa munthu, osati okonda Mulungu.” Ana adzakhala “osamvela akuwabala.” (2 Timoteo 3:1-5) Kodi simuvomeleza kuti masiku ano pali anthu ambili amene ali conco? Iwo alibe ulemu kwa Mulungu, ndipo amavutitsa aja amene amafuna kuphunzila za Mulungu.

Kucita zaupandu. Kudzakhalanso ‘kuculuka kwa kusaweluzika.’ (Mateyu 24:12) Ngakhale imwe mungavomeleze kuti masiku ano zaupandu zimacitika kwambili kusiyana na kale. Anthu kulikonse amaopa kuŵabela, kuŵanama kapena kuŵapweteka.

Zonse izi zionetsa kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Baibo imakamba kuti: “Pakuona zinthu izi zilikucitika, zindikilani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:31) Kodi Ufumu wa Mulungu ni ciyani? Ni boma yakumwamba imene idzabweletsa Paladaiso padziko lino lapansi. Ufumu wa Mulungu ukabwela udzacotsapo maboma onse a anthu.—Danieli 2:44.