Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kanani Cipembedzo Conama!

Kanani Cipembedzo Conama!

Phunzilo 11

Kanani Cipembedzo Conama!

Satana na viŵanda vake safuna kuti imwe muzitumikila Mulungu. Iwo amafuna kuti acotse munthu aliyense ku mbali ya Mulungu ngati angakwanitse. Kodi amayesa kucita zimenezi kupitila mu njila za bwanji? Imodzi mwa njila zimenezo ni cipembedzo conama. (2 Akorinto 11:13-15) Cipembedzo ciliconse cimene cimaphunzitsa zimene sizicokela mu Baibo ni conama. Cipembedzo conama cili monga ndalama yabodza—ngakhale kuti ingaoneke monga ni yazoona, imakhala ilibe nchito. Ingakubweletseleni mavuto akulu.

Mabodza a cipembedzo sangakondweletse Yehova, Mulungu wa coonadi. Pamene Yesu anali padziko lapansi, panali anthu ena acipembedzo amene anafuna kumupha. Anali kuona kuti cipembedzo cawo ndiye cinali coona. Iwo anakamba kuti: “Tili naye tate mmodzi ndiye Mulungu.” Kodi Yesu anavomeleza zimenezo? Kutalitali! Koma iye anawauza kuti: “Inu muli ocokela mwa atate wanu Mdyelekezi.” (Yohane 8:41, 44) Anthu ambili masiku ano amaganiza kuti amalambila Mulungu, koma kwenikweni amatumikila Satana na viŵanda vake!—1 Akorinto 10:20.

Monga mmene mtengo umene uli na matenda umabalila zipatso zoipa, cipembedzo conama cimakhala na anthu ocita voipa. Padziko lapansi pali mavuto ambili cifukwa ca vinthu voipa vimene anthu amacita. Pali uhule, kumenyana, kuba, kupondelezana, kuphana, na kugona akazi mokakamiza. Ambili amene amacita vinthu ivi ali na cipembezo cawo, koma cipembedzo cawo siciwalimbikitsa kucita zinthu zabwino. Kuti akhale anzake a Mulungu afunikila kuleka kucita voipa.—Mateyu 7:17, 18.

Cipembedzo conama cimaphunzitsa anthu kupemphela ku mafano. Mulungu amaletsa kupemphela ku mafano. Ndipo zimenezi ni zomveka. Mwacitsanzo, kodi mungamve bwanji ngati munthu wina, m’malo mokamba na imwe, amakamba cabe na cithunzithunzi kapena cipikica canu? Kodi mungakambe kuti munthu ameneyo ni mnzanu wazoona? Iyai. Conco, Yehova amafuna kuti anthu azikamba naye, osati kukamba na cifanizilo copanga kapena cipikica cimene cilibe moyo.—Eksodo 20:4, 5.

Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti si kulakwa kupha anthu pankhondo. Yesu anakamba kuti anzake a Mulungu adzakhala okondana pakati pawo. Ife sitingaphe anthu amene timakonda. (Yohane 13:35) Ngakhale kupha anthu oipa ni kulakwa. Pamene adani a Yesu anabwela kuti amumange, iye sanalole kuti ophunzila ake amenyane nawo kuti amucinjilize.—Mateyu 26:51, 52.

Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti anthu oipa adzapsa m’mulilo ku helo. Koma Baibo imaphunzitsa kuti ucimo umapeleka ku imfa. (Aroma 6:23) Yehova ni Mulungu wacikondi. Nanga Mulungu wacikondi angaoche anthu m’moto kwamuyaya? Iyai, sangacite zimenezo. Mu Paladaiso mudzakhala cipembedzo cimodzi cabe, cimene Yehova amavomeleza. (Cibvumbulutso 15:4) Mulungu adzaononga vipembedzo vonse vimene vimaphunzitsa mabodza a Satana.