Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 88

Yohane Abatiza Yesu

Yohane Abatiza Yesu

ONA nkhunda imene ibwela pamutu pa mwamuna uyu. Mwamuna ameneyu ni Yesu. Iye tsopano ali ndi zaka pafupi-fupi 30. Ndipo wina uyu amene ali naye ni Yohane. Tinaphunzilapo kale za Yohane ameneyu. Kodi ukumbukila pamene Mariya anayenda kukacezela wacibanja wake Elizabeti, ndipo mwana amene anali m’mimba mwa Elizabeti analumpha cifukwa ca kukondwela? Mwana amene uja anali Yohane. Koma kodi Yohane ndi Yesu tsopano acita ciani?

Yohane wambiza Yesu m’madzi a mu mtsinje wa Yorodano. Umu ni mmene munthu amabatizidwila. Coyamba, munthu amamuloŵetsa thupi lonse m’madzi, ndiyeno amamutulutsa. Popeza Yohane amabatiza anthu, ndiye cifukwa cake amachedwa Yohane Mbatizi. Koma n’cifukwa ciani Yohane abatiza Yesu?

Yohane anacita zimenezi cifukwa Yesu anabwela kwa iye ndi kumupempha kuti amubatize. Yohane amabatiza anthu amene afuna kuonetsa kuti alapa zoipa zimene anali kucita. Koma kodi Yesu anacita coipa ciliconse cimene anafunikila kulapa? Iyai, Yesu sanacitepo coipa ciliconse, cifukwa ni Mwana weni-weni wa Mulungu wocokela kumwamba. Conco anapempha Yohane kuti amubatize pa cifukwa cina. Tiye tione kuti n’cifukwa ciani.

Yesu asanabwele kwa Yohane, anali mmisili wamatabwa kapena kuti kalipentala. Kalipentala ni munthu amene amapanga zinthu monga mathebulo, mipando ndi mabenchi mogwilitsila nchito matabwa, kapena kuti mapulanga. Yosefe, mwamuna wa Mariya, anali mmisili wamatabwa, ndipo anaphunzitsako Yesu nchito imeneyo. Koma Yehova sanatume Mwana wake padziko lapansi kuti adzakhale kalipentala. Iye ali ndi nchito yapadela yakuti aicite, ndipo nthawi yafika yakuti Yesu ayambe kugwila nchito imeneyo. Conco, kuonetsa kuti tsopano wayamba kucita cifunilo ca Atate wake, Yesu apempha Yohane kuti amubatize. Kodi Mulungu akondwela ndi zimenezi?

Inde akondwela nazo, cifukwa pamene Yesu atuluka m’madzi, pamveka mau ocokela kumwamba akuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga, amene nimakondwela naye.’ Komanso kumwamba kutseguka, ndipo nkhunda itsikila pa Yesu. Imeneyi si nkhunda yeni-yeni, koma kweni-kweni ni mzimu woyela wa Mulungu.

Yesu tsopano ali ndi zambili zoganizila, conco apita ku malo akwayekha kwa masiku 40. Ali kumeneko, Satana amufikila. Katatu konse Satana ayesa kucititsa kuti Yesu aphwanye malamulo a Mulungu. Koma Yesu sangacite zimenezo.

Pambuyo pake, Yesu abwelela kukakumana ndi amuna amene adzakhala otsatila kapena ophunzila ake oyamba. Maina a ena a io ni Andireya, Petulo (wochedwanso Simoni), Filipo ndi Natanayeli (wochedwanso Batolomeyo). Yesu ndi ophunzila ake atsopano apita ku cigao ca Galileya. Ali kumeneko, aima mu mzinda wa Kana, kwao kwa Natanayeli. Ndiyeno Yesu apita kuphwando lalikulu la cikwati, ndipo kumeneko acita cozizwitsa cake coyamba. Kodi ucidziŵa cozizwitsa cimeneci? Asandutsa madzi kukhala vinyo.