Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 54

Munthu Wamphamvu Kwambiri

Munthu Wamphamvu Kwambiri

KODI umudziŵa munthu wamphamvu kwambili amene anakhalako padziko lapansi? Ni woweluza, ndipo dzina lake ni Samsoni. Yehova ndiye anapatsa mphamvu Samsoni. Pamene Samsoni akalibe kubadwa, Yehova auza amai ake kuti: ‘Posacedwa udzakhala ndi mwana mwamuna. Ndipo adzatsogolela ndi kupulumutsa Aisiraeli kucokela kwa Afilisti.’

Afilisti ni anthu oipa amene akhala mu dziko la Kanani. Iwo ali ndi amuna ankhondo ambili ndipo acitila nkhanza Aisiraeli. Nthawi ina pamene Samsoni ayenda kumene Afilisti akhala, akumana ndi cimkango cikulu colusa. Koma Samsoni akupha cimkango cimeneci ndi manja ake. Ndipo akuphanso Afilisti ena oipa okwana mahandeledi.

Potsilizila pake, Samsoni akondana ndi mkazi wina dzina lake Delila. Atsogoleli a Afilisti alonjeza kuti aliyense wa io adzapatsa Delila ndalama za siliva zokwana 1,100, ngati iye adzawauza cimene cimapangitsa Samsoni kukhala wamphamvu kwambili. Delila afunitsitsa ndalama zimenezo. Iye si mnzake weni-weni wa Samsoni, kapena anthu a Mulungu. Conco, apitiliza kumunyengelela kuti amuuze cimene cimamupangitsa kukhala wamphamvu kwambili.

Potsilizila pake, Samsoni auza Delila cisinsi ca mphamvu zake. Iye akamba kuti: ‘Tsitsi langa likalibe kugeledwapo, kucokela nthawi imene n’nabadwa, Mulungu ananisankha kukhala mtumiki wake wapadela wochedwa Mnazili. Akanigela tsitsi, mphamvu zanga zidzatha.’

Pamene Delila amvela zimenezi, agonetsa Samsoni mu tulo pamiyendo pake. Ndiyeno aitana mwamuna wina kuti aloŵe amugele tsitsi. Pamene Samsoni auka, apeza kuti mphamvu zake zatha. Ndiyeno Afilisti abwela ndi kumugwila. Iwo amuboola maso ndi kumupanga kapolo wao.

Tsiku lina Afilisti anali ndi phwando lalikulu lolambila mulungu wao Dagoni, ndipo anacotsa Samsoni mu ndende kuti azimuseka. Apa tsitsi la Samsoni linakulanso. Ndiyeno Samsoni anauza kamnyamata kamene kanali kumuyendetsa kuti: ‘Nigwilitse vipilala vimene vagwila nyumba ino.’ Samsoni apemphela kwa Yehova kuti amupatse mphamvu, ndipo agwila molimba vipilala vija. Ndiyeno afuula kwa Yehova kuti: ‘Nifele nao pamodzi Afilisiti awa.’ Pa phwando limeneli pali Afilisiti 3,000, ndipo pamene Samsoni aŵelamila mwamphamvu vipilala, nyumba ija ikugwa ndi kupha anthu onse oipa amenewo.

Oweruza mu macaputa 13-16.