UMOYO WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Pafoni
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Ulaliki wa pafoni ni njila yabwino yocitila “umboni mokwanila za uthenga wabwino.” (Mac. 20:24) * Ulaliki wa pafoni umatipatsa mwayi wolalikila munthu amene mikhalidwe yathu sitilola kumufikila mwacindunji.
MMENE TINGACITILE:
-
Konzekelani. Sankhani nkhani yoyenelela. Ndiyeno lembani mwacidule zimene mufuna kukamba. Mungakonzekelenso uthenga wacidule umene mungakambe ngati mwina mwatumila munthu amene amaseŵenzetsa cipangizo coyankha cokha mafoni. Cimakhala bwino kukhala pa thebulo muli na tumawu tumene mwalemba komanso zinthu zina zofunikila, monga foni, tabuleti, kapena kompyuta ili yotsegula JW Laibulali® kapena jw.org®
-
Khalani omasuka. Kambani mwacibadwa. Muzimwetulila na kucita magesica monga kuti munthuyo akukuonani. Pewani kudula-dula mawu popanda zifukwa zomveka bwino. Cimakhala bwino kucita ulalikiwu pamodzi ndi anthu ena. Ngati mwininyumba wafunsa funso, libwelezeni mokweza kuti mnzanu amene mulalikila naye akuthandizeni kupeza yankho
-
Yalani maziko a ulendo wobwelelako. Ngati munthuyo ali na cidwi, mungamusiile funso lokayankha nthawi yotsatila mukakamutumilanso. Mungamupemphenso kuti mumutumile cofalitsa pafoni olo pakompyuta, kukamupelekela cofalitsaco, kapena kumutumizila kupitila ku positi ofesi. Mwinanso mungamupemphe kuti mumutumizile imodzi mwa nkhani kapena mavidiyo athu. Ngati m’poyenela, muuzeni za Maphunzilo a Baibo a pa Intaneti kapena zinthu zina zopezeka pa webusaiti yathu.
^ ndime 3 Ngati ulaliki wa pa foni ni wovomelezeka m’dela lanu, muyenela kuucita mogwilizana na malamulo oteteza zinthu zaumwini.