UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pitilizani Kugaŵila Magazini
Kuyambila mu 2018, magazini iliyonse yogaŵila imafotokoza pa nkhani imodzi cabe. Magazini onsewa ni mbali ya zida zophunzitsila za mu Thuboksi yathu. Conco tiyenela kuwaseŵenzetsa mu ulaliki. Komanso tinganyamuleko magazini angapo ngati tili pa ulendo kapena popita kukagula zinthu. Colinga ca magaziniwa si kutsogozela phunzilo la Baibo. Ngakhale n’conco, angapangitse munthu kukhala na cidwi na uthenga wathu.
Mukayambitsa makambilano, ŵelengani lemba na kuchula nkhani ya m’magazini imene munthuyo angacite nayo cidwi. Mwacitsanzo, ngati ali na ŵana kapena ali na cisoni kapena nkhawa, mungakambe kuti: “Posacedwapa, n’naŵelengapo nkhani inayake yothandiza pa mbali imeneyi. Kodi mungakonde kuiona?” Ngati munthuyo waonetsa cidwi, mungamugaŵile magazini yopulintidwa kapena mungamutumizile pa foni kapena pa tabuleti yake. Mungacite zimenezi olo kuti ni ulendo woyamba. Ngakhale kuti colinga cathu cacikulu si kugaŵila zofalitsa, kugaŵila magazini kungatithandize kupeza anthu amene amafuna kucita zimene aphunzila.—Mac. 13:48.
2018
2019
2020
Kodi anthu m’gawo lanu amacita cidwi na nkhani ziti?