Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 14-15

Kulambila Koona Kumafuna Kukhala Oyela

Kulambila Koona Kumafuna Kukhala Oyela

15:13-15, 28-31

Kuti Mulungu apitilize kutikonda, tiyenela kukhala oyela mkati na kunja komwe. Izi zitanthauza kuti timayesetsa kutsatila mfundo za Yehova zimene zimafuna kuti tizikhala aukhondo, a khalidwe loyela, komanso osaipitsidwa mwauzimu, mosasamala kanthu za khalidwe la anthu amene tikhala nawo. Timapewa kukhudza ciliconse cimene Atate wathu wakumwamba amati n’codetsedwa.

Kodi timapindula bwanji ngati tipewa kutsatila mfundo zimene anthu m’dzikoli amayendela?