Onani zimene zilipo

Kodi Ufumu wa Mulungu Uli mu Mtima Mwanu?

Kodi Ufumu wa Mulungu Uli mu Mtima Mwanu?

Yankho la m’Baibo

 Ayi. Ufumu wa Mulungu suli mu mtima mwa Mkhristu. * Baibo imachula malo enieni amene Ufumuwu umapezeka. Imati “ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 4:17) Onani mmene Baibo imaonetsela kuti Ufumuwu, ni boma lenileni limene likulamulila kucokela kumwamba.

  •   Ufumu wa Mulungu uli na olamulila, nzika zake, malamulo, komanso uli na colinga cakuti cifunilo ca Mulungu cicitike kumwamba ndiponso padziko lapansi.—Mateyu 6:10; Chivumbulutso 5:10.

  •   Boma la Mulungu, kapena kuti Ufumu, lidzalamulila ‘anthu a mitundu yosiyana-siyana, komanso olankhula zinenelo zosiyana-siyana’ padziko lonse lapansi. (Danieli 7:13, 14) Mphamvu za olamulila a Ufumuwu zimacokela kwa Mulungu osati kwa nzika zake.—Salimo 2:4-6; Yesaya 9:7.

  •   Yesu anauza atumwi ake okhulupilika kuti ‘adzakhala m’mipando yacifumu’ pamodzi naye mu Ufumu wakumwamba.—Luka 22:28, 30.

  •   Ufumuwu udzawononga adani ake onse.—Salimo 2:1, 2, 8, 9; 110:1, 2; 1 Akorinto 15:25, 26.

 Baibo siiphunzitsa kuti Ufumu wakumwamba uli mu mtima mwanu, kapena kuti umalamulila mu mtima wa munthu. Komabe, imaonetsa kuti “mawu a Ufumu” kapena ‘uthenga wabwino wa ufumu’ umatha kusintha mtima wa munthu.—Mateyu 13:19; 24:14.

Kodi mawu akuti “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu” atanthauza ciani?

 Anthu ena akaŵelenga m’ma Baibo ena pa Luka 17:21, amasokonezeka pa nkhani ya malo amene kuli Ufumu wa Mulungu. Mwacitsanzo, Baibo yakuti Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, limati “Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu.” Koma kuti timvetse molondola vesiyi, tiyenela kukhala na cithunzi ca nkhani yonse.

Ufumu wa Mulungu sunali m’mitima ya anthu oipa amene anatsutsa Yesu mpaka kufipa pomupha

 Apa Yesu anali kukamba na Afarisi, amene anali gulu la atsogoleli acipembedzo amene anali kumutsutsa, komanso amene anakonza ciwembu cakuti amuphe. (Mateyu 12:14; Luka 17:20) Kodi muona kuti zingakhale zomveka kukamba kuti Ufumu wa Mulungu unali m’mitima ya anthu oipa amenewo? Yesu anawauza kuti: “Mkati mwanu mwadzaza cinyengo ndi kusamvela malamulo.”—Mateyu 23:27, 28.

 Ma Baibo ena anamasulila momveka bwino mawu a Yesu apa Luka 17:21 amenewa, kuti: “Ufumu wa Mulungu uli na imwe pano.” (Ndife tapendeketsa mawuwo; Contemporary English Version) “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” (Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika) Ufumu wakumwamba unali “pakati” pa Afarisiwo cifukwa Yesuyo, amene anasankhidwa na Mulungu kukhala Mfumu, anali pakati pawo.—Luka 1:32, 33.

^ ndime 1 Zipembedzo zambili zacikhristu zimaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu uli mu mtima mwa munthu. Mwacitsanzo, msonkhano wina wacipembedzo ca Baptist ku America, unalengeza kuti mbali ya Ufumu wa Mulungu ni “ulamulilo wa Mulungu mu mtima komanso pa umoyo wa munthu.” Mofananamo, m’buku lake lakuti Jesus of Nazareth, Papa Benedict wa nambala 16 anati “Ufumu wa Mulungu umabwela mwa munthu akakhala na mtima womvetsela.”