Onani zimene zilipo

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani Yocotsa Mimba?

Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani Yocotsa Mimba?

Yankho la m’Baibo

 Baibo siigwilitsa nchito mawu akuti “kucotsa mimba” ponena za kupha mwana wosabadwa. Komabe, malemba ambili aonetsa mmene Mulungu amaonela moyo wa munthu, kuphatikizapo wa mwana wosabadwa.

 Moyo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. (Genesis 9:6; Salimo 36:9) Iye amaona kuti moyo wa cinthu ciliconse ni wamtengo wapatali, kuphatikizapo moyo wa mwana amene akali m’mimba mwa mayi ake. Conco, wina akapha mwana wosabadwa mwadala, n’cimodzimodzi na kupha munthu.

 Mulungu anapatsa Aisiraeli lamulo lakuti: “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambili mkazi wapakati moti mkaziyo n’kubeleka mwana koma palibe amene wamwalila, wovulaza mkaziyo azimulipilitsa ndithu malinga ndi zimene mwiniwake wa mkaziyo angagamule. Azikapeleka malipilowo kudzela mwa oweluza. Ngati wina wamwalila, pamenepo uzipeleka moyo kulipila moyo.”—Ekisodo 21:22, 23. *

 Kodi moyo wa munthu umayamba liti?

 Mulungu amaona kuti moyo wa mwana umayamba mayi akangotenga pakati. M’Baibo, Mulungu amaonetsa mobweleza-bweleza kuti mwana amene sanabadwe ni munthunso payekha. Onani zitsanzo zotsatilazi, zimene zionetsa kuti Mulungu amaona kuti palibe kusiyana pakati pa moyo wa mwana amene ali m’mimba na mwana amene wabadwa kale.

  •   Mothandizidwa na mzimu woyela, Mfumu Davide anauza Mulungu kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” (Salimo 139:16) Mulungu anaona kuti Davide ni munthu ngakhale pamene anali asanabadwe.

  •   Komanso, Mulungu anadziŵilatu kuti mneneli Yeremiya adzakhala na utumiki wapadela, Yeremiyayo asanabadwe. Mulungu anamuuza kuti: “Ndisanakuumbe m’mimba, ndinakudziŵa, ndipo usanatuluke m’mimbamo, ndinakusankha kuti ucite nchito yopatulika. Ndinakusankha kuti ukhale mneneli ku mitundu ya anthu.”—Yeremiya 1:5.

  •   Luka amene analemba nawo Baibo komanso amene anali dokotala, anaseŵenzetsa mawu a Cigiriki amodzimodzi akuti “khanda” ponena za mwana wosabadwa, komanso ponena za mwana wobadwa kumene.—Luka 1:41; 2:12, 16.

 Kodi Mulungu angakhululukile munthu amene anacotsapo mimba?

 Inde. Mulungu akhoza kukhululukila anthu amene anacotsapo mimba. Ngati anasintha n’kumaona moyo mmene Mulungu amauonela, sayenela kumadziimba mlandu. Baibo imati: “Yehova ndi wacifundo ndi wacisomo . . . Monga mmene kum’mawa kwatalikilana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikila kutali zolakwa zathu.” * (Salimo 103:8-12) Yehova amakhululukila anthu onse amene anacitapo macimo, kuphatikizapo kucotsa mimba ngati alapa kucokela pansi pa mtima.—Salimo 86:5.

 Kodi n’kulakwa kucotsa mimba ngati moyo wa mayi kapena wa mwana uli pa ciwopsezo?

 Mogwilizana na zimene Baibo imakamba pa nkhani ya mwana wosabadwa, kungakhale kulakwa kwakukulu ngati mayi atacotsa mimba cifukwa cakuti wauzidwa kuti moyo wake kapena wa mwanayo uli pangozi.

 Nanga bwanji ngati pa nthawi yobeleka papezeka mavuto ena amene zivute zitani mukufunika musankhe pakati pa kupulumutsa moyo wa mayi kapena wa mwana? Zikakhala conco, aliyense ayenela kusankha yekha kuti kaya kupulumutsa moyo wake kapena wa mwanayo.

^ ndime 3 Mabaibo ena amamasulila lamuloli m’njila yakuti zizioneka ngati cofunika kwambili cinali moyo wa mayiyo, osati moyo wa mwana wosabadwayo. Koma m’Chiheberi, lembali limanena za kuphedwa kwa onse, mayi kapena mwana.

^ ndime 8 Yehova ni dzina la Mulungu, ndipo limapezeka m’Baibo.—Salimo 83:18.