Onani zimene zilipo

Kodi Mulungu Alikodi?

Kodi Mulungu Alikodi?

Yankho la m’Baibo

 Inde, Baibo imapeleka umboni wokhutilitsa wakuti Mulungu aliko. Ndipo imatilimbikitsa kuika cikhulupililo cathu mwa Mulungu, komanso kuseŵenzetsa “luntha la kuganiza,” na “nzelu” zathu, m’malo mongokhulupilila ziphunzitso zilizonse za cipembedzo. (Aroma 12:1; 1 Yohane 5:20) Onani maumboni otsatilawa ocokela m’Baibo:

  •   Kukhalapo kwa cilengedwe conse mwadongosolo cimene cili na zamoyo, ni umboni wakuti kuli Mlengi. Baibo imati: “N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheberi 3:4) Ngakhale kuti mfundo imeneyi ni yosavuta kumvetsa, anthu ophunzila kwambili amati ni mfundo yamphamvu kwambili. *

  •   Ise anthu, mwacibadwa tili na cikhumbo cofuna kumvetsetsa colinga ca moyo, ndipo cikhumbo cimeneci sicimatha ngakhale titakhala na zinthu zonse zakuthupi. Zimenezi ni zina mwa zinthu zimene Baibo imazichula kuti ‘zosowa zathu zauzimu,’ zimene zimaphatikizapo cikhumbo cathu cofuna kudziŵa Mulungu na kum’lambila. (Mateyu 5:3; Chivumbulutso 4:11) Cikhumbo cimeneci ni umboni wakuti Mulungu alikodi, komanso kuti ni Mlengi wacikondi amene amafuna kuti cikhumbo cathuco cikhutilitsidwe.—Mateyu 4:4.

  •   Maulosi ambili a m’Baibo analembedwa zaka mahandiledi pasadakhale, koma anakwanilitsidwa ndendende mmene ananenedwela. Kulondola kwake kwa mbali iliyonse ya maulosi amenewa, ni umboni wamphamvu wakuti anacokeladi kwa Mulungu.—2 Petulo 1:21.

  •   Olemba Baibo anali kudziŵa mfundo zina zokhudza sayansi zimene anthu ena apanthawi yawo sakanatha kuzimvetsetsa. Mwacitsanzo, m’zaka zamakedzana anthu ambili anali kukhulupilila kuti dziko lapansi linakhazikika pa nyama inayake monga njovu, ngulube, kapena ng’ombe. Mosiyana na zimenezi, Baibo imaonetsa kuti Mulungu “anakoloweka dziko lapansi m’malele”. (Yobu 26:7) Komanso, Baibo imafotokoza molondola maumbidwe a dziko lapansi kuti ni “lozungulila,” kapena kuti “lobulungila.” (Yesaya 40:22, mawu am’munsi; Douay Version) Anthu oculuka amaona kuti mafotokozedwe omveka a mfundo yozama imeneyi, ni yakuti olemba Baibo anali kucita kuuzilidwa na Mulungu.

  •   Baibo imayankha mafunso ovuta ambili, amene ngati munthu sanapeze mayankho okhutilitsa angayambe kukhulupilila kuti Mulungu kulibe. Mwacitsanzo: Ngati Mulungu ni wacikondi komanso wamphamvu zonse, n’cifukwa ciani padziko pali mavuto ambili conco? N’cifukwa ciani zipembedzo kaŵili-kaŵili zimasonkhezela zinthu zoipa m’malo mwa zinthu zabwino?—Tito 1:16.

^ ndime 2 Mwacitsanzo, wasayansi wina wa zakuthambo dzina lake Allan Sandage, ponena za cilengedwe iye anakamba kuti: “Niona kuti sizoona kuti dongosolo ili m’cilengedwe inangocitika mwangozi. Pafunika kukhala winawake anacita zimenezi. Ine sinikhulupilila kuti kuli Mulungu, koma kukhalapo kwa mlengi ndiko kokha kungafotokoze mmene cilengedwe cinakhalilako, cifukwa kukanakhala kulibe ciliconse popanda mlengi.”