Onani zimene zilipo

N’cifukwa Ciyani a Mboni za Yehova Satengako Mbali pa Zikondwelelo Zonyadila Dziko Lawo?

N’cifukwa Ciyani a Mboni za Yehova Satengako Mbali pa Zikondwelelo Zonyadila Dziko Lawo?

 A Mboni za Yehova amalemekeza maboma na zizindikilo za dziko lawo. Timavomelezanso kuti anthu ali na ufulu wosankha kucitila saliyuti mbendela kapena kuimba nyimbo ya fuko.

 Komabe, a Mboni za Yehovafe siticitako nawo miyambo imeneyi cifukwa timakhulupilila kuti imasemphana na ziphunzitso za m’Baibo. Timayamikilanso ngati anthu ena alemekeza zimene timakhulupilila, monga mmene ifenso timalemekezela zawo.

Zimene zili m’nkhani ino

 Kodi tili na zifukwa zanji za m’Baibo?

 Cisankho cathu pa nkhaniyi catsamila pa mfundo ziŵili izi za m’Baibo:

  •   Tiyenela kulambila Mulungu yekha cabe. Baibo imakamba kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.” (Luka 4:8) Kambili, nyimbo ya fuko imakhala na mawu olonjeza kukhulupilika ku dziko lako kuposa ku cina ciliconse. Pa cifukwa cimeneci, cikumbumtima ca a Mboni za Yehova siciŵalola kucitako zinthu zimenezi, monga kuimba nyimbo ya fuko.

     A Mboni za Yehova amaonanso kuti kucitila saliyuti mbendela ni cimodzi-modzi na kupembedza, kapena kulambila mafano, kumene Baibo imaletsa. (1 Akorinto 10:14) Akatswili ena amavomeleza kuti m’ceniceni mbendela za maiko ni zizindikilo za kulambila. “Cizindikilo cacikulu ca cikhulupililo ca konda dziko lako ni mbendela,” anatelo wolemba mbili yakale dzina lake Carlton J. H. Hayes. a Pokamba za Akhristu oyambilila, wolemba mabuku wina, dzina lake Daniel P. Mannix, anati: “Akhristu anakana . . . kupeleka nsembe kwa mzimu wa mfumu [ya Roma]—zomwe zikufanana na kukana kucitila saliyuti mbendela masiku ano.” b

    Ngakhale kuti ife a Mboni za Yehova siticitila saliyuti mbendela, sitivomeleza kuwononga mbendela, kuiwocha, kapena kunyozela cizindikilo ca dziko lililonse.

  •   Anthu onse ni olingana pamaso pa Mulungu. (Machitidwe 10:34, 35) Baibo imati “kucokela mwa munthu mmodzi, [Mulungu] anapanga mitundu yonse ya anthu.” (Machitidwe 17:26) Ndiye cifukwa cake a Mboni za Yehova, amaona kuti n’kulakwa kukweza mtundu wina, kapena kuona kuti dziko lina n’lapamwamba kuposa ena. Timalemekeza anthu onse mosayang’ana kumene akucokela kapena kumene amakhala.—1 Petulo 2:17.

 Bwanji ngati lamulo la boma likufuna kuti titengeko mbali?

 A Mboni za Yehova si otsutsa boma. Timakhulupilila kuti maboma alipo mololedwa na Mulungu, ndipo ni mbali ya “zimene Mulungu anakonza.” (Aroma 13:1-7) Timakhulupililanso kuti Akhristu ayenela kumvela akulu-akulu a boma.—Luka 20:25.

 Koma bwanji ngati malamulo a boma awombana na malamulo a Mulungu? Nthawi zina n’zotheka kupempha boma kuti lisintheko malamulo ena. c Koma ngati boma lakana kusinthako lamulo, mwaulemu a Mboni za Yehova amasankha “kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Machitidwe 5:29.

 Kodi colinga ca Mboni za Yehova ni kutsutsa Boma?

 Iyayi. Mboni za Yehova sizikhalila mbali m’zandale. Tikakana kucitila saliyuti mbendela kapena kuimba nyimbo ya fuko, sindiye kuti tikutsutsana na boma ayi. M’malo mwake, timakhala tikutsatila mfundo za m’Baibo zimene timakhulupilila pa nkhani ya miyambo imeneyi.

a Buku lakuti Essays on Nationalism, masamba 107-108.

b Buku lakuti The Way of the Gladiator, masamba 212.