Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 7

Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

(Yesaya 12:2)

  1. 1. M’lungu wathu ndimwe mphamvu zathu.

    Imwe ndimwe mpulumutsi wathu.

    Timalengeza uthenga wanu,

    Ngakhale kuti ena samvela.

    (KOLASI)

    Yehova ndimwe wamphamvuzonse.

    Timadziŵitsa dzina lanu.

    Yehova timakudalilani.

    Ndimwe mphamvu zathu—nsanja yathu.

  2. 2. Mwationetsa kuwala kwanu.

    M’lungu mwatiphunzitsa co’nadi.

    Mu Mau anu tipeza nzelu;

    Ise tasankha Ufumu wanu.

    (KOLASI)

    Yehova ndimwe wamphamvuzonse.

    Timadziŵitsa dzina lanu.

    Yehova timakudalilani.

    Ndimwe mphamvu zathu—nsanja yathu.

  3. 3. Timatumikila mokondwela,

    Ngakhale Satana ‘tivutitse.

    Ngakhale tikumane na imfa

    Ise tidzamvela imwe cabe.

    (KOLASI)

    Yehova ndimwe wamphamvuzonse.

    Timadziŵitsa dzina lanu.

    Yehova timakudalilani.

    Ndimwe mphamvu zathu—nsanja yathu.

(Onaninso 2 Sam. 22:3; Sal. 18:2; Yes. 43:12.)