Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 140

Moyo Wosatha Watheka!

Moyo Wosatha Watheka!

(Yohane 3:16)

  1. 1. Mokondwa timaona

    Mu maganizo mwathu,

    Paradai’so yafika,

    Sitivutikanso.

    (KOLASI)

    Imba mokondwela!

    Tamanda Yehova.

    Sangalala

    Cifukwa ca moyo wosatha.

  2. 2. Matenda, ukalamba,

    Yehova adzacotsa.

    Imfa nayo si’liko

    Kulibe cisoni.

    (KOLASI)

    Imba mokondwela!

    Tamanda Yehova.

    Sangalala

    Cifukwa ca moyo wosatha.

  3. 3. Tonsefe, panthawiyo,

    Tidzatamanda M’lungu.

    Nthawi zonse, mokondwa,

    Tidzamuimbila.

    (KOLASI)

    Imba mokondwela!

    Tamanda Yehova.

    Sangalala

    Cifukwa ca moyo wosatha.

(Onaninso Yobu 33:25; Sal. 72:7; Chiv. 21:4.)