Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 104

Mphatso ya Mzimu Woyela

Mphatso ya Mzimu Woyela

(Luka 11:13)

  1. 1. Mfumu, Yehova, Atate wathu,

    Ndinu Mulungu wacifundo.

    Tithandizeni, titonthozeni,

    Kuti tilimbane na mavuto.

  2. 2. Inu mudziŵa ndise ocimwa;

    Nthawi zina timasocela.

    Conde mvelani pemphelo lathu.

    Titetezeni na mzimu wanu.

  3. 3. Tikavutika, tikakhumudwa

    Mzimu wanu uticengete.

    M’lungu tipempha, tilimbitseni,

    Tipitilize kucilimika.

(Onaninso Sal. 51:11; Yoh. 14:26; Mac. 9:31)