Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Military equipment: Anton Petrus/Moment via Getty Images; money: Wara1982/iStock via Getty Images Plus

KHALANI MASO!

Ndalama Matililiyoni Zawonongedwa pa Nkhondo—Koma Kodi ni Ndalama Zokha Zawonongeka?

Ndalama Matililiyoni Zawonongedwa pa Nkhondo—Koma Kodi ni Ndalama Zokha Zawonongeka?

 Nkhondo ni cinthu cowononga zedi.

  •   “Caka catha maboma padziko lonse anawononga ndalama zokwana madola 2.2 tililiyoni a ku America pa nkhondo zingapo. Uku n’kuyamba maiko kugwilitsa nchito ndalama zoculuka conci pa nkhondo m’caka cimodzi.”—Inatelo nyuzipepala ya The Washington Post, pa February 13, 2024.

 Koma si ndalama zokha zimene zawonongeka. Mwacitsanzo, onan’koni zina zimene zawonongeka pa nkhondo ya ku Ukraine.

  •   Asilikali. Akatswili ena akukhulupilila kuti asilikali pafupifupi 500,000 aphedwa kapena kuvulazidwa ciyambileni nkhondoyi zaka ziŵili zapitazi.

  •   Anthu wamba. Malinga na bungwe la United Nations, anthu wamba oposa 28, 000 aphedwa kapena kuvulazidwa. Komabe, mmodzi wa akulu-akulu m’bungwe la UN anakamba kuti: “N’zosatheka kudziŵa ciŵelengelo ceniceni ca anthu omwe aphedwa pa nkhondo yowononga imeneyi.” a

 Mavuto amene anthu akukumana nawo cifukwa ca nkhondo ni aakulu kwambili.

  •   114 miliyoni. Ici n’ciŵelengelo ca padziko lonse ca anthu amene anakakamizika kuthawa kwawo cifukwa ca nkhondo na zaciwawa pofika mu September 2023.

  •   783 miliyoni. Ici n’ciŵelengelo ca anthu amene alibe cakudya cokwanila. “Nkhondo ndiyo vuto lalikulu limene lapangitsa kuti pakhale kucepekela kwa cakudya. Padziko lonse, 70 pelesenti ya anthu amene alibe cakudya cokwanila amakhala m’madela amene muli nkhondo na za ciwawa.”—Linatelo bungwe la World Food Programme.

 Kodi nkhondo zidzathadi? Kodi pali ciyembekezo ciliconse cakuti padzikoli padzakhala mtendele? Kodi kudzakhalako nthawi pamene munthu aliyense sadzavutika na njala komanso umphawi? Kodi Baibo imatipo ciyani?

Nthawi ya nkhondo

 Baibo inakambilatu kuti kudzakhala nkhondo m’madela osiyanasiyana pa dzikoli. Inayelekezela nkhondo na wokwela pa hachi, kapena kuti hosi.

  •   “Panatuluka hachi ina yofiila ngati moto. Amene anakwela pahachi imeneyi analoledwa kucotsa mtendele padziko lapansi, kuti anthu aphane ndipo anapatsidwa lupanga lalikulu.”—Chivumbulutso 6:4.

 Wokwela pa hosi wophiphilitsa ameneyu atapita, panabwela okwela pa mahachi ena aŵili amene akuimila njala komanso imfa yobwela cifukwa ca milili kapena zinthu zina. (Chivumbulutso 6:5-8) Kuti mudziŵe zambili za ulosi wa m’Baibo umenewu, komanso cifukwa cake tingakhale otsimikiza kuti ukukwanilitsika masiku ano, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?

Tsogolo la mtendele

 Posacedwa, cuma ca m’dziko sicidzagwilitsidwanso nchito pa nkhondo. Koma si anthu amene adzacititsa zimenezi. Baibo imati:

  •   Mulungu adzathetsa “nkhondo padziko lonse lapansi.”—Salimo 46:9.

  •   Mulungu adzathetsa mavuto obwela cifukwa ca nkhondo. “Iye adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

  •   Mulungu adzaonetsetsa kuti anthu onse akukhala mwamtendele. “Anthu anga adzakhala pamalo amtendele, adzakhala pamalo otetezeka komanso pamalo abata ndi ampumulo.”—Yesaya 32:18.

 Malinga na maulosi a m’Baibo, nkhondo na mavuto ena amene akucitika masiku ano ni umboni wakuti nthawi ya mtendele imeneyi yayandikila.

 Kodi Mulungu adzaseŵenzetsa ciyani kuti abweletse mtendele padziko? Adzaseŵenzetsa Ufumu wake wa kumwamba umene ni boma. (Mateyu 6:10) Kuti mudziŵe kuti Ufumu umenewu n’ciyani komanso zimene ungakucitileni, tambani vidiyo yaifupi yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciyani?

a Miroslav Jenca, wothandizila kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations ku Europe, pa December 6, 2023.