Anton Petrus/Moment via Getty Images

KHALANI MASO!

Kodi Nkhondo Ina ya Padziko Lonse Yatsala Pang’ono Kucitika?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Kodi Nkhondo Ina ya Padziko Lonse Yatsala Pang’ono Kucitika?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 M’zaka 30 zapitazi, anthu ambili anali kuona kuti maiko ali pa mtendele komanso kuti ni ogwilizana. Koma zocitika zaposacedwapa zionetsa kuti umu si mmene zinthu zilili.

  •   “Anthu ali na nkhawa yakuti nkhondo ya ku Gaza idzakhudzanso maiko ena ozungulila, cifukwa dziko la Israel na gulu lochedwa Hezbollah ayamba kuthilana nkhondo ku malile a dziko la Lebanon.”—Reuters, January 6, 2024.

  •   “Magulu otsogoleledwa na dziko la Iran akuukila madela osiyanasiyana. Ndipo dziko la Iran layambanso zoyesayesa zake zofuna kupanga zida za nyukiliya. Kuwonjezela apo, maiko a Russia na China apanga mgwilizano na dzikolo. Zocitika zonsezi zikubweletsa ciopsezo ku maiko a Azungu.”—The New York Times, January 7, 2024.

  •   “Dziko la Russia lapitilizabe kuukila na kusakaza dziko la Ukraine.”—UN News, January 11, 2024.

  •   “Kupita patsogolo kwa dziko la China pa zacuma komanso pa zankhondo, kuwonjezeka kwa mzimu wokonda dziko lawo ku Taiwan, komanso kusagwilizana kwa dziko la China na America, zingapangitse kuti mkangano ubuke mosavuta.”—The Japan Times, January 9, 2024.

 Kodi Baibo imakambapo ciliconse pa kusagwilizana kwa maiko kumene tikuona m’dzikoli? Kodi izi zingayambitse nkhondo ina ya padziko lonse?

Baibo inakambilatu zimene zikucitika masiku ano

 Baibo sinakambiletu za nkhondo ina iliyonse imene ikucitika masiku ano. Komabe, inakambilatu zakuti kudzakhala nkhondo zoculuka monga mmene tikuonela masiku ano. Nkhondo zimenezi “[zikucotsa] mtendele padziko lapansi.”—Chivumbulutso 6:4.

 Buku la Danieli linanenelatu kuti “m’nthawi yamapeto,” maulamulilo amphamvu padziko lonse ‘adzakankhana’ kapena kuti kulimbilana ulamulilo. Linanenanso kuti pa kukankhana kumeneku, maiko adzaonetsa mphamvu zawo zazikulu pa zankhondo na kuwononga “cuma” coculuka.—Danieli 11:40, 42, 43.

Nkhondo imene ikubwela

 Baibo imaonetsa kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino padzikoli. Koma nthawiyo isanafike, zinthu zidzafika poipa kwambili. Yesu anakambilatu kuti “kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela paciyambi ca dziko.” (Mateyu 24:21) “Cisautso cacikulu” cimeneco cidzayambitsa nkhondo yochedwa Aramagedo, imene ni “[nkhondo] ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 16:14, 16.

 Nkhondo ya Aramagedo sidzawononga mtundu wonse wa anthu, m’malomwake idzaupulumutsa. Pa nkhondo imeneyo, Mulungu adzathetselatu maboma onse a anthu, amene acititsa kuti pa dzikoli pacitike nkhondo zambili zowononga. Kuti mudziŵe mmene Aramagedo idzabweletsela mtendele wosatha, ŵelengani nkhani zotsatilazi: