Onani zimene zilipo

‘Palibe Ngakhale Mawu Amodzi Omwe Sanakwanilitsidwe’

Ulendo wa Aisiraeli wa m’cipululu unali utatha, ndipo Dziko Lolonjezedwa limene anali kuliyembekezela kwa nthawi yaitali linali kuonekela. Kodi Aisiraeli, amene panthawiyo anali kutsogoleledwa ndi Yoswa, akanamvela Yehova ndi mtima wonse ndi kulandila madalitso amene Iye anawalonjeza? Nkhani imeneyi ingakuthandizeni kukhulupilila kwambili kuti zimene Mulungu analonjeza zidzakwanilitsidwa.