Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kodi moyo uno ndiwo wokha umene ulipo?

Kodi nthawi zina mumaona kuti moyo ndi waufupi?

Kodi munadzifunsapo kuti colinga ca moyo ndi kusangalala, kugwila nchito, kukwatila kapena kukwatiwa, kulela ana ndi kukalamba basi? (Yobu 14:​1, 2) Baibulo limaonetsa kuti ngakhale anthu anzelu kwambili anafunsapo funso limeneli.​—Ŵelengani ­Mlaliki 2:​11.

Kodi moyo uli ndi phindu lililonse? Kuti tiyankhe funso limeneli coyamba tifunse kuti, Kodi moyo unayamba bwanji? Poona mmene bongo wathu ndi thupi lathu zinapangidwila, ambili azindikila kuti pali Mlengi wanzelu amene anatipanga. (Ŵelengani Salimo 139:14.) Ngati zili conco, ndiye kuti pali cifukwa cimene anatipangila. Kudziŵa cifukwa cimeneco kungatithandize kuona kuti moyo uli ndi colinga.

N’cifukwa ciani Mulungu anapanga anthu?

Mulungu anadalitsa anthu aŵili oyambilila ndi kuwapatsa nchito yosangalatsa kwambili. Iye anafuna kuti anthuwo akhale ndi moyo kosatha, adzaze dziko ndi kulisandutsa kukhala paladaiso.​—Ŵelengani Genesis 1:​28, 31.

Colinga ca Mulungu cinasokonezeka pamene anthu anapandukila ulamulilo wake. Koma ngakhale zinali conco, Mulungu sanatikane ndipo sanasinthe colinga cake pa anthu ndi dziko lapansi. Baibulo limatitsimikizila kuti Mulungu wakhala akugwila nchito kuti apulumutse anthu ake okhulupilika ndi kuti colinga cake cokhudza dziko lapansi cidzakwanilitsidwa. Conco, Mulungu afuna kuti mudzasangalale ndi moyo wabwino umene anafuna poyamba. (Ŵelengani Salimo 37:29.) Baibulo limatiuza mmene inuyo mudzapindulila ndi colinga ca Mulungu cimeneci.