Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Phunzilani Zimene Mawu a Mulungu amanena

Kodi pa Tsiku la Ciweluzo Padzacitika Zotani?

Kodi pa Tsiku la Ciweluzo Padzacitika Zotani?

Nkhani ino ili na mafunso amene mwina mumafuna mutadziŵa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ni okonzeka kukambilana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Tsiku la Ciweluzo limatanthauza ciani?

Monga tikuonela pacithunzi cili kumanjaci, anthu ambili amaganiza kuti pa Tsiku la Ciweluzo anthu onse adzaonekela pampando wacifumu wa Mulungu ndipo adzaweluzidwa malinga na nchito zimene anacita. Anthuwa amaganiza kuti ena adzalandila moyo kumwamba ndipo ena adzapita kukazunzidwa kumoto. Koma Baibo imasonyeza kuti colinga ca Tsiku la Ciweluzo ni kupulumutsa anthu ku zinthu zopanda cilungamo zimene zimacitika padzikoli. (Salimo 96:13) Mulungu wasankha Yesu kukhala Woweluza wake amene adzabweletsa cilungamo kwa anthu.—Ŵelengani Yesaya 11:1-5; Machitidwe 17:31.

2. Kodi Tsiku la Ciweluzo lidzabwezeletsa bwanji cilungamo padzikoli?

Pamene munthu woyamba Adamu anacimwila Mulungu mwadala, anacititsa kuti anthu onse akhale ocimwa, azivutika komanso azifa. (Aroma 5:12) Kuti zinthu zibwelelenso mmene zinalili poyamba, Yesu adzaukitsa anthu ambili-mbili amene anamwalila. Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti zimenezi zidzacitika pa nthawi yaulamulilo wa Yesu Khristu wa zaka 1,000.—Ŵelengani Chivumbulutso 20:4, 11, 12.

Anthu amene adzaukitsidwewo sadzaweluzidwa potengela zimene anacita asanamwalile, koma zimene adzacite ataukitsidwa mogwilizana na zimene zidzalembedwe “m’mipukutu” yomwe yachulidwa mu Chivumbulutso caputala 20. (Aroma 6:7) Mtumwi Paulo ananena kuti anthu “olungama ndi osalungama omwe” adzaukitsidwa. Anthu amenewa adzapatsidwa mwayi wophunzila za Mulungu.—Ŵelengani Machitidwe 24:15.

3. Kodi pa Tsiku la Ciweluzo padzacitika zotani?

Anthu onse amene anamwalila asanaphunzile za Yehova Mulungu na kumutumikila, adzapatsidwa mwayi wophunzila za Yehova. Ngati iwo adzasankhe kutumikila Mulungu, ndiye kuti adzakhala kuti ‘anauka kuti alandile moyo.’ Komabe ena mwa anthu oukitsidwawo sadzafuna kuphunzila za Yehova kuti azimutumikila. Anthu otelewa adzakhala kuti ‘anauka kuti aweluzidwe.’—Ŵelengani Yohane 5:28, 29; Yesaya 26:10; 65:20.

Kumapeto kwa Tsiku la Ciweluzo, lomwe lidzakhale la zaka 1,000, Yehova adzabwezeletsa anthu omvela kukhalanso angwilo monga mmene Adam na Hava analili poyamba. (1 Akorinto 15:24-28) Cimeneci ni ciyembekezo cosangalatsa kwambili comwe anthu omvela ali naco. Kenako, Mulungu adzamasula Satana Mdyerekezi kuphompho komwe adzakhala atamangidwa kwa zaka 1,000. Satana akadzamasulidwa, adzayesa anthu kuti asatumikile Yehova ndipo amene adzakane kusoceletsedwa naye adzakhala na moyo wosatha padziko lapansi.—Ŵelengani Yesaya 25:8; Chivumbulutso 20:7-9.

4. Kodi ni tsiku lina liti laciweluzo limene lidzabweletsa madalitso kwa anthu?

Baibo imachulanso “tsiku lina laciweluzo” ponena zimene zidzacitika Mulungu akamadzawononga anthu oipa padzikoli. Tsiku laciweluzo limeneli lidzabwela modzidzimutsa monga mmene cinabwelela Cigumula ca Nowa cimene cinawononga anthu onse oipa. Kuwonongedwa kwa “anthu osaopa Mulungu,” kudzacititsa kuti padzikoli ‘pakhale cilungamo.’—Ŵelengani 2 Petulo 3:6, 7, 13.